Apolisi atolera matumba a simenti okwana 186 ku Mchinji


People stole bags of cement after a truck was involved in an accident last month

Apolisi m’boma la Mchinji ati matumba a simenti okwana 186 ndi omwe apezeka pakadali pano pa matumba okwana 600 kutsatira pomwe thilaki yomwe idanyamula matumbawa idayaka moto kwa Kholoni mbomali.

Thilakiyi yomwe ndi ya kampani ya Fermak idanyamula matumba a kampani ya AgriCom yomwe nambala yake ndi NS 1751 komanso telera yake ndi NS 5282 idayaka moto lachinayi pomwe imalowera ku Lilongwe komwe imakatsitsa matumbawa.

Panthawiyo dalayivala wa thilakiyi adadabwa pomva mfungo lakupsa kwachinthu. Apa adayimitsa kaye thilakiyi kuti awone mpamene adapeza kuti ku boneti ya injini kudali kutayaka moto.

Iye adayesetsa kuzimitsa motowo ndichozimitsira koma sizidaphule kanthu. Dalayivalayo adapulumuka pangoziyo popanda kuvulala koma galimotolo lidapsera pompo mpakana phulusa

Anthu ena anapezerapo mwayi pa ngoziyi ndikutenga matumba a simenti.

Apolisi m’bomali adatsinidwa khutu za nkhaniyi ndipo adayamba kufufuza matumbawa khomo ndi khomo ndipo matumba 186 ndi omwe apezekapo koma ntchito yofufuza ikadali mkati.