Mbava zitatu zomwe zimaba pobisalira gulewamkulu azilamula kukaseweza jere


Njonda zitatu zomwe zidanjatidwa pa mlandu okuba katundu zitavala ngati gulewamkulu kwa Chaima m’boma la Kasungu azipeza zolakwa pa mlandu wakuba ndipo  azilamula kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka 12.

Nkhani yonse ikuti njondazi  zitatuzi zomwe ndi a Sadarack Phiri azaka 48 zakubadwa, a Lazaro Nkhoma azaka 47  ndi a John Mkula azaka 35 anabera mnyamata wina yemwe dzina lake ndi Solomon Samuel.

Njondazo zinaba njinga ya kapalasa, chimanga cholemera ma kilogiramu 40 komanso ndalama zokwana K30,000 ali mugulewamkulu.

Akubawa atagwidwa, anaonekera ku bwalo la milandu la Kasungu First Grade Magistrate komwe anatemetsa nkhwangwa pamwala kuwukana mlanduwu.

Apa a Clement Bwanali yemwe ndi woyimira boma anasonkhanitsa mboni zitatu zomwe zinaperekera umboni kufikira njondazi zinapezeka zolakwa pa mlandu wakuba.

Njonda zitatuzi  ndi za m’dera ya mfumu yaying’ono Chaima m’boma la Kasungu.

Wolemba: Ben Bongololo