Apolisi ku Machinga akhazikitsa makomiti owona zachitetezo cha m’madera


Community Policing Forum Members in Machinga

Apolisi m’boma la Machinga akhazikitsa makomiti owona zachitetezo cha m’madera a kumidzi m’bomalo pofuna kuchepetsa umbava ndi umbanda munyengo ino yachikondwelero cha khirisimasi komanso chaka chatsopano.

Poyankhula pamwambo omwe amakhadzikitsa komiti yowoona zachitetedzo chamadera akumudzi mdera la T/A Mtumbwinda mkulu woona zachitetedzo chamadera akumudzi ku Police ya Machinga Masautso Katemera walangiza komiti yatsopanoyo kuti idzigwira ntchito yawo mokhulupilika komanso motsatira malamulo.

Sub-Inspector Katemera adati cholinga chokhadzikitsa makomiti owoona zachitetezo chamadera akumidzi ndikufuna kuti umbava ndi umbanda usamachitike m’madera mwao choncho adawuza komitiyo kuti iwonetsetse kuti idziteteza katundu wa anthu kuti asamabedwe komanso adzikanena ku police akawona anthu odabwitsa kapena omwe akuwakayikira kuti akuchita za umbanda ndi umbava.

Pamenepa iwo adapereka uthenga wochokera kwa Mkulu wa a Police Boma la Machinga Senior Assistant Commissioner Jane Mandala wofunira zabwino komiti yatsopanoyo pomwe ikuyamba kugwira ntchito yawo ndipo adati a police a bomalo adzigwira nawo ntchito limodzi yozungulira m’delaro masana ndi usiku komanso awonetsetsa kuti awapatse zida zogwilira ntchito.

“Chitetezo chidziyamba ndi inu eni ake ndipo mudziwonetsetsa kuti mukumazungulira kupereka chitetezo koma chomwe ndingakupempheni ndi choti musamachite zachinyengo chifukwa aliyense opezeka akuchita zachinyengo lamulo lidzagwira ntchito,” adatero Sub Inspector Katemera.

Mu mau ake, T/A Mtumbwinda adathokoza apolisi a Boma la Machinga chifukwa chokhazikitsa ubale wabwino ndi anthu amdera lake.

Mfumu Mtumbwinda adati ngati mfumu ikhala patsogolo kugwira ntchito limodzi ndi komiti yatsopanoyo yopereka chitetedzo mdera lake.

Poyankhulanso, wapampando woona zachitetedzo chamadera akumidzi m’oma la Machinga a Richard Kalasa adawuza komiti yatsopanoyo kuti akhale patsogolo kugwira ntchito yopereka chitetezo komanso apewe kuchita milandu ina iliyonse pofuna kuti komiti yawo isakhale ndi mbiri yoyipa

Komiti yatsopanoyo itangotsankhidwa idalandira maphunziro amomwe angamagwilire ntchito yawo komanso komitiyo idalandira zovala usiku (refrector jackets) zoti azivala pogwira ntchito yawo.