Anthu atatu afa galimoto itagudubuzika

Advertisement

Anthu atatu amwalira pamene anthu ena asanu ndi m’modzi avulala pa ngozi yomwe yachitika dzulo madzulo m’boma la Nkhotakota

Yemwe ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Sub-Inspector Andrew Kamanga ati galimoto ya mtundu wa Sienta yomwe inanyamula anthuwa inagudubuzika itanyamula anthuwa munsewu wa M5.

A Aaron Cement omwe amayendetsa galimotoli komanso wolandira ndalama m’galimotoli ndi mwana wa zaka khumi ndi omwe afa pangoziyi.

Ovulalawa anathamangira nawo kuchipatala mbomali komwe akulandira thandizo.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement