Mphunzitsi wanjatidwa kamba kobela anthu ponena kuti ndi wapolisi


Malawi Teacher

A polisi mu mzinda wa Lilongwe ku Area 3, anjata  a Jonathan Nkhosa yemwe ndi mphunzitsi wa kupulayimale wa zaka 51 zakubadwa, kamba kobera anthu powanamiza kuti ndi wapolisi.

A Nkhosa akhala akuchita bodza kwa abale a anthu omwe ali mkusungidwa mchitokosi cha apolisi powauza kuti alipire ndalama kuti m’bale wawo atuluke pa belo.

Yemwe ndi wachiwiri kwa mneneri wa a polisi mu mzinda wa Lilongwe a constable Khumbo Sanyiwa wati  a Nkhosa awanjata pomwe iwo amanyengelera mkulu wina kuti apereke ndalama kuti m’bale wawo atuluke pa belo.

Koma mkuluyo anazemba ndikukatsina khutu wa CID wina pa zankhaniyi.

Wachiwiri kwa m’neneri wa apolisiyu watinso iwo akhala akulandira malipoti ankhaninkhani kuti anthu ena akumabera anzawo powanamiza kuti alipire ndalama kuti atuluke pa belo.

Mphunzitsiyu amachokera m’boma la Lilongwe m’mudzi mwa Bwemba kwa mfumu yayikulu Kalolo ndipo akuyembekezereka kukayankha mulandu obera anthu powanamiza kuti ndi wa polisi.

Wolemba: Ben Bongololo