Tay Grin osadzaonekera ndi zingongo zako m’mutu, watero Mutale


Mutale Mwanza Zambian socialite in Malawi

Omwe ukumveka ndi kuoneka kuti ndi ubwezi pakati pa oyimba odziwika bwino mdziko muno Tay-Grin ndi mayi odziwika bwino wa mdziko la Zambia wafika pa m’nong’a pamene mayiyu wauza Nyau king kuti asapite kokaonekera ndi zingongo m’mutu.

Polemba pa tsamba lake, Mutale Mwanza wati iye akulonjeza kudzakhala mayi wabwino wa ana a awiriwa ndipo amasangalatsidwa Tay-Grin akameta osati ndi zitsekero za botolo m’mutu.

“Mukamete Simukubwera kudzakumana ndi a kubanja a kwathu ndi zitsekelero za botolo m’mutu mwakomo,” walemba choncho Mwanza mu chizungu.

Masiku apitawa, awiriwa akhala akuoneka m’miseu ya dziko lino komanso akhala akuoneka akusangalala limodzi m’malo osiyanasiyana komanso kunyanja

Awiriwa akhalanso akukumana ndi ena mwa anthu odziwika bwino monga mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi, Nduna yowona zokopa alendo a Vera Kamtukule mwa ena.