Boma alipempha kuti lichite changu popeleka zipangizo za ulimi


Phungu wa nyumba ya malamulo wa dera lapakati mu mzinda wa Lilongwe Alfred Jiya wapempha boma kuti lichite machawi popeleka zipangizo za ulimi zotsika mitengo kwa anthu okhala m’madera amatawuni ponena kuti nawo ali ndi minda komanso amafuna kukhala ndi chakudya chokwanila.

Iye walakhula izi m’nyumba ya malamulo lachiwiri sabata ino pomwe anafunsa funso nduna ya zaulimi Sam Kawale momwe ntchito yopeleka zipangizo zaulimi zotsika mitengo yikuyendela.

Mwazina Jiya wati nawo anthu am’matawuni ali ndi minda choncho akuyenera kukhala ndi danga lopeza zipangizozi.

“Kwenikweni kunali kupempha Kwa Anduna chifukwa mukawona bwino bwino mupeza kunena kuti madera a ma tawuni mumasalidwa nthawi zambiri komanso tawuniyo ngakhale imatchedwa tawuni ili ndi mbali ina imeneso ili yayikulu imene ili kumudzi. Anthu akumudziwa amapanga chinachilichonse ngati akumudzi ali ndi Minda yomwe amalima. Ndiye anthu amenewa akuyenera ataganizilidwa mu nthawi yoyenelela,” iwo anatero.

Poyakhapo pa nkhaniyi, nduna ya zaulimi a Sam Kawale ati anthu am’matawuni asadele nkhawa ndipo apindula ndi ndondomekoyi pomwe tsopano akutsiliza kupelekera zipangizo zaulimi zotsika mitengo m’madera ovuta kufika.