Anthu aja afika ku Israel, akuti kuno za mamangidwe timangonamizana


Israel Malawians

..akuti Nankhumwa amafuna awakhomelele

A Malawi oposa 200 omwe anali paulendo aja, afika m’dziko la Israel ndipo ati ndiokozeka kukhala ma tenanti koma akutitu ukuku kuli nyumba zosanjikizana mbwelekete ndipo akuti kuno ku mpanje timangonamizana pa nkhani ya mamangidwe komaso ati anakakonda a Lazarus Chakwera anakapita nawo kuti akaone mamangidwe apamwambawo.

Ndege yomwe yanyamula anthuwa yomwe ndiya aRKIA Airbus a321-251NX, Iinagwira tambala pakhosi pochoka m’dziko muno pomwe malipoti akusonyeza kuti inanyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe mma 1 kololo m’bandakucha wa lero loweruka.

Itangodutsa nthawi yankhomaliro patsikuli, zithunzi komaso makanema owonetsa anthuwa ali m’dziko la Israel, anali mbwelekete pamasamba anchezo osiyanasiyana ndipo anthu ochuluka m’dziko muno athokoza Mulungu kuti anthuwa ayenda bwino mlengalenga.

Ena mwa makanema omwe atenga malo kwambiri ndimonga yomwe ikumawaonetsa anthuwa akutsika ndege yomwe anakwera ndipo ina ndi yomwe ikumawaonetsa anthuwa akuvina kwina ku akuyimba; “Nankhumwa mukumva kuwawa ehh Mukumva kupweteka. Mumatinena kuti sitibwela, lero tabwela, mumva m’bebe.”

Koma zosezo nchabe, kanema amene watenga mitima ya anthu ndipo akuwoneledwa pafupifupi ndi yemwe akuonetsa anthuwa ali mlengalenga ndipo anayamikira mamangidwe pomwe amadutsa malo ena momwe ndege yawo inatsala pang’ono kutera m’dziko la Israel.

Anthu angapo akuveka mu kanemayi akuyankhula motamanda nyumba zosanjikizana zomwe zili m’dziko la Israel ndipo polephera kusimba wati ku Malawi kuno tinakali kutali pa nkhani ya za mamangidwe.

Munkucheza kwawo, anthuwa analoza chala mtsogoleri wa mbali yotsutsa mu nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa ponena kuti amafuna kuwalepheletsera ulendo wawo ndipo munthu wina so anati anakakonda Chakwera anakapita ku ulendowu kuti akaone nyumba za pamwambazi.

“Tawonani kuno kuli nyumba ngati ya Kang’ombe zanbirimbiri, zomangidwa ngati Reserve bank zambirimbiri. Kwathu kuja tinyumba 10 basi akuti tawuni. Eeeh ma guy Malawi tinakali kutali kwambili, ndipo sitinayambe ndipo tikunamamizana kwambiri kumenekuja.

“Pulezidenti amafunikaso abwere nawo adzaone mamangidwe omwe ali kuno. Kunoku nde ku Tiyeni Tiyeni Tiyeni! Osati kuja timanenena kuja. Kuteleku Nankhumwa amafuna atikhomelere zimenezo? Aaaa Nankhumwa amajoka (joking) kwambiri eti?” Amavomelezana a Malawi-wo ali mu ndege.

Kutchulidwa kwa a Nankhumwa, ndikamba koti iwo lachiwiri anabenthura kuti m’dziko muno mukuyembekezeka kufika ndege kuchokera m’dziko la Israel kudzatenga achinyamata 221 kuti akagwire ntchito zakumunda mu dziko la Israel.

Patsikuli Nankhumwa anapempha unduna wa za ntchito kuti ufotokoze chilungamo chenicheni pa za ntchito yomwe achinyamata akukagwira mu dziko la Israel ponena kuti panaliso mphekesera kuti achinyamatawa akukamenya nkhondo ya dziko la Israel ndi dziko la Palestine.

Izi zinabweretsa mapokoso m’nyumba ya malamuloyi kamba koti akuluakulu ambali ya boma anapempha a Nankhumwa kuti abweze zomwe ayankhulazi ndikubweretsa umboni weniweni wa nkhaniyi.