Bambo ndi mwana afa atadya chilazi

Advertisement
Malawi24.com

Anthu awili m’boma la Balaka afa atadya zomwe iwo amaganizira kuti ndi chilazi.

Anthu omwe afawa ndi bambo wazaka 50 ndi mwana wake wa zaka 17.

Izi zadza pamene athuwa amadya zikhawo chifukwa chanjala kamba kakuti sadakolore chimanga chokwanira..

A Wongani Nyirenda omwe ndi ndi m’neri wa chipatala chachikulu cha Machinga atsimikiza ndipo ati bambo ndi mwanayu afa kamba ka poizoni.

A Asiyatu Mwamadi omwe ndi achitatu pobadwa m’nyumbamo anafotokoza kuti mwana wa zaka 17, ndiye anayamba kumwalira.

Iwo anati bambowa amwalira mchipatala ku Machinga akulandira thandizo.

Anthuwa amachokera m’mudzi mwa Chim’dikiti m’boma la Balaka

Wolemba: Ben Bongololo, Salima

Advertisement