MEC yalimbikitsa anthu a Ntiya Ward kuti adzaponye voti

Advertisement

M’modzi wa makomishonala a bungwe lomwe limawona zachisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) a Caroline Mfune apempha anthu a mdera la Ntiya Ward mu Mzinda wa Zomba kuti adzaponye voti yosankha Khansala wa kumtima kwawo pachisankho chomwe chikuyembekezeka kudzachitika pa 26 September chaka chino.

A Mfune adayankhula izi mu Mzinda wa Zomba pomwe amayendera m’malo omwe bungweli lakhazikitsa kuti anthu omwe akuyenera kudzavota adzikawona mayina awo mukawundula.

Iwo adati m’malo onse omwe ayendera awona kuti palibe china chilichonse chomwe chavuta ndipo anthu akubwera kudzawona maina awo.

Iwo adalimbikitsa anthuwo kuti adzapite kukaponya voti yosankha Khansala pachisankho chachibwerezachi popeza chitukuko sichingabwere ngati kulibe woyimilira pankhani yopempha zitukuko zosiyanasiyana ku Khonsolo.

Pamenepa komishonala Mfune adati anthu a mdera la Ntiya Ward akhala nthawi yayitali opanda Khansala choncho adawalangiza kuti asadzanyozere kukaponya vote pa 26 September mwezi wammawa.

“Chitukuko sichingabwere ku Ward komwe kulibe Khansala popeza iye ndiye mwini chitukuko choncho kusaponya vote ndiye kuti mukudzimana nokha chitukuko,” Adatero Commissioner Caroline Mfune.

Chisankho chachibwereza chichitika ku Ward ya Ntiya mu Mzinda wa Zomba pa 26 September potsatira kumwalira kwa Khansala Ramsey Kajosolo yemwe adali wachipani cha UTM.

Advertisement