Wamisala adawona nkhondo: kapena JB ankanena zoona? Anthu akufusana za Onesimus

Advertisement
Onesimus Malawi

M’modzi mwa oyimba odziwika bwino m’dziko muno, Onesimus, wadzetsa manong’onong’o m’masamba a nchezo kaamba ka zovala zomwe anavala komaso kupezeka kwake ku phwando lomwe anakonza ndi yemwe amadziwika ndi za ‘umgochana’, Somizi.

Somizi Mhlongo wa m’dziko la South Africa yemwe ndi muwulutsi wa pa wailesi ya kanema komaso ochita masewero, anapangitsa phwando loweluka pa 19 August, 2023 pa malo otchedwa Centre Court, Emperors Palace m’dzikolo.

Somizi analitchula phandoli ‘Shades of Pink’ zomwe zimatanthauza kuti aliyese opita ku malowo ayenera kuvala zovala za makaka a pinki, omwe anthu amati zovala za makakawa amayenera kuvala ndi akazi.

Chitsitsa dzaye nchakuti Somizi ndi m’modzi mwa anthu omwe amadziwika bwino pa nkhani ya anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha ngakhale kuti chaka chatha anakana za mphekeserazi.

Mophiphilitsa, Somizi anauza dziko kuti iye samagonana ndi amuna anzake koma anati iye amasangalatsidwa ndi munthu aliyese posatengera kuti ndi wa nkazi kapena mamuna.

Kupezeka kuphwandoli kwa Onesimus yemwe anabadwa Armstrong Kalua kwautsa mapili pa chigwa kaamba koti posachedwapa Jolly Bro yemwe ali m’dziko la America anauza anthu kuti oyimba nzakeyu amachita nawo za “umgochana”.

JB anati anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha alipo ambiri mdziko muno ndipo anauza aMalawi kuti asalore kuti mwikho umenewu usefukire kuno ku Malawi.

“Zithunzi zayamba kutuluka apapa za anyamata otiwa tsitsi. Anthu awa ndikagulu, apapa nde kuti amuimbira Sibusiso wa ku Joni uja, homo uja, mwankumbukira?” anatelo JB.

Pakadali pano a Malawi ochuluka m’masamba a nchezo ayamba kukumbutsana za zomwe anayankhula JB zokhudza Onesimus ndipo anthu ochuluka ati ndizodandaulitsa ngat mphekeselazi zili zowona.

“Wa Ganyu can now confirm that Onesimus Muzik is a gay (mngochana) as already indicated by JB and today they’re attending shades of pink hosted by the famous gay in South Africa Somizi,” anatelo munthu wina pa fesibuku.

Anthu ochuluka omwe ayikira ndemanga zithunzi zomwe Onesimus anayika pa tsamba lake la fesibuku zomwe anavomeleza kuti analidi nawo ku phwando lomwe anakoza Somizi, ati oyimbayu wakhala ngati Agalatiya opusa.

“Sibasi mwaziika poyera? sitifunaso umboni wina, apa nde Agalatiya enienitu, munayamba bwino koma mhuu. Eee Mulungu atichitile chifundo ndithu,” watelo munthu wina yemwe anayankha za zithuzi zomwe Onesimus anaika.

Munthu wina walangiza Onesimus kuti angobwera poyera ndikuliuza dziko kuti iye amachita nchitidwe wa mathanyula.

“Pang’onong’ono muzaulura… I know that for now it’s your conscious which keeps pushing you back but mtima wanu umafuna mutatulukira poyera,” anateloso munthu wina.

Advertisement