Madzi okhalitsa amanunkha — Chilima

Advertisement

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima dzulo anayankhula ndi a Malawi ku Mzuzu dzulo komwe anapereka miyambi.

A Chilima anafika mu mzindawu dzulo pa ndege ndipo analandilidwa ndi chikhamu cha anthu chomwe chinasonkhana pa pafupi ndi Mzuzu Shoprite.

Mu mawu awo a Chilima anapeleka miyambi iwir.

Oyamba ndi oti “Moto okonza pa kona umawotcha chipupa” ndipo wachiwiri unali wa mchitumbuka onena kuti “Maji ghakukhaliska ghakununkha (Madzi okhalitsa amanunkha)”.

A Chilima sanalankhulepo pa za mavuto a zachuma omwe a Malawi akukumana nawo pansi pa ulamuliro wa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera mothandizidwa ndi iwowo a Chilima.

Ku Mzuzu a Chilima akhala nawo lero pa mwambo odzodza a Yohane Suzgo Nyirenda ngati wansembe wa Mzuzu Diocese ya tchalichi cha Katolika.

Ku mwambowu kukhalanso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera omwe anapita ku Mzuzu lachinayi.

Mwambowu ukuchitika patangotha masiku ochepa a Chilima atakaonekera ku khoti ku Lilongwe pa mlandu wawo woti analandira ndalama zosachepera K300 milliyoni kuchokera kwa a Zuneth Sattar.

Advertisement