Mwalephera, tisankhe atsogoleri ena chaka chino – atelo mamembala a NGC ya DPP

Advertisement
Peter Mutharika is the president of the Democratic Progressive Party and former President of Malawi

…ati NGC siyinasankhe a Mutharika

Mamembala ena akomiti yayikulu ya chipani cha DPP (NGC) akupitilira kuwulura zakutsimba ndipo ati mtsogoleri wawo Peter Mutharika walephera kuyendetsa bwino chipanichi choncho sakuyenera kudzionjezera nthawi yolamulira.

Izi ndi malingana a Baxtor Kita omwe mogwilizana ndi a Werani Chilenga komaso a Simeon Phiri, anachititsa msonkhano wa atolankhani Lolemba mumzinda wa Lilongwe komwe amakafotokoza zina mwa zomwe zinamanga nthenje ku mkumano wa akuluakulu a chipani cha DPP posachedwapa.

A Kita anayamba ndikudandaula kuti zambiri ku msonkhano omwe unachitika ku Mangochi masabata awiri apitawo sizinayende bwino zomwe ati zili ndikuthekera kupangitsa chipanichi kulowa pansi kwambiri m’dziko muno ngat zimene anawonazo zingapitilire kuchitika.

“Chipani sichikhala cha anthu ochepa, anthu atatu, chimakhala cha dziko lonse la Malawi ndipo ngati pali chipani chomwe anthu akuyembekeza kuti chikulowa m’boma ndi chipani cha DPP. DPP ngati ikuyembekeza kulowa m’boma imayenera iyambiletu kupanga zinthu zolongosoka, chiyambe kudzikoza chokha chisadalowe m’boma. Boma kuti liyende bwino chipani cholamulacho chimafunika chikhale organized,” anayamba choncho a Kita.

Iwo anati anali odabwa kuti mkumano wawo ku Mangochi unangoyamba osapeleka mwayi kwa anthu kuti adzitchule maina komaso maudindo awo m’chipani ndipo awulura kuti kumeneko kunali anthu ena omwe si mamembala a NGC ya DPP.

A Kita ati anthu ku mkumanowu sanapatsidwe mpata opeleka maganizo pa malamulo atsopano omwe chipanichi chikufuna kukhazikitsa zomwe anati sizikuyenera kuchitika mu nthawi ino ya ulamuliro wa zipani zambiri, demokalase.

Iwo adzudzula mtsogoleri wa chipanichi a Mutharika kuti akukakamira udindo pamene alephera kuyendetsa chipani ndipo ati sizoyenera kuti chipani cha DPP chichititse nsonkhano wawukulu mu July chaka cha mawa.

“Chifukwa chochedwetsera kuti mpaka tidzavoteso chaka cha mawa mu July ndi chiyani? Anthu ambiri akuti mukutiphwanyira ufulu. Simunapange pelefomu (perfom) koma mungodzionjezela nokha telemu kwa chaka china chifukwa chiyani?. Palibe chifukwa chodzavotera mpaka cha mawa.

“Pali kuthekera koti tikhala ndi mtsogoleri watsopano. Ameneyo akuyenera ayambe kukoza chipani kuti kugawanika konse komwe kuli mchipani kuthe, abweretse chipani pamodzi, ayambe kuchikonza kuti tikamafika chaka cha mawa chipani chikhale chili pamodzi mkumapanga kampeni mkumapita” anateloso a Kita.

Iwo anatsindikaso kuti zomwe akuyankhulazo sikuti akudana ndi a Mutharika koma ati akufuna kuti aliyese azitsata malamulo a chipani posatengera udindo umene munthuyo ali nawo mchipanimo.

Mbali inayi a Chilenga omwe anaufotokoza msonkhanowu ngati odabwitsa kwambiri iwo chiyambileni ndale, ati iwo pamodzi ndi anthu ena ankafuna kuyankhula kunkumanowo koma sanapatsidwe mpata otelo.

A Chilenga ati anthu ochuluka anali odabwa ndi zomwe a Chipiliro Mpinganjira anayankhula zoti mamembala a NGC awatuma kuti awapemphe a Mutharika kuti adzaimileso chipanichi pa chisankho cha dziko mu 2025.

“Ine ndapanga nawo ma meeting ochuluka koma iyi inali yodabwitsa kwambiri kwa ine. Kunalibe kudzifotokoza kuti tidziwe kuti tonse tinalidi ma membala a NGC. A Nsonda ankafuna kuyankhula koma anthu ena anamukuwiza kuti akhale pansi. Ine ndinkafunaso ndiyankhule koma ndinauzidwa kuti tipatsidwa nthawi tiyankhula koma sizinachitike.

“China chodabwitsa chinali choti pa agenda panilibe zoti tipanga endorse munthu. Tinadabwa kuti nthawi yamathokozo Chipiliro Mpinganjira akunena kuti anthu amutuma kuti apulezidenti ayimeso koma zinali zochita kupanga iwowo. Kumusankha Mutharika sanalakwitse koma analakwitsa kunena kuti yasankha ndi NGC,” anatelo a Chilenga.

Akuluakuluwa ati ndiodandaula kuti mpaka pano chipanichi chitulukireni m’boma, sichinakhale pansi ndikukambirana zoyenera kuchita komaso kuwunikirana mmene analephelera pa zisankho za mchaka cha 2020.

Iwo apemphaso mtsogoleri wa chipanichi kuti abweretse poyera chibuku cha mfundo zomwe akufuna kuti zisinthidwe malamulo a chipanichi.

Advertisement