Chakwera akupita ku China lero

Advertisement

Zonse zili mchimake kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anyamuke kupita mdziko la China komwe akukakhala mlendo olemekezeka pa chionetsero cha za malonda cha China – Africa Economic and Trade Expo (CAETE).

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe unduna woona za ubale wa dziko lino ndi mayiko ena watulutsa dzulo lolemba chomwe chikutsimikiza za ulendo wa mtsogoleri wa dzikoyu.

Malingana ndi chikalatachi, a Chakwera pamodzi ndi mayi wa pfuko, Monica, anyamuka lero pabwalo la ndege la Kamuzu mumzinda wa Lilongwe nthawi ya kota pasiti 2 masana (14:15) kupita mumzinda wa Changsha mchigawo cha Hunan m’dziko la China.

A Chakwera akuyenera kukayankhula pa chionetsero cha malonda cha CAETE chomwe chikuyembekezeka kuyamba pa 29 June mpaka pa 2 July chaka chino ndipo undunawu wati ulendowu ndiwofunika kwambiri kaamba koti aka kakhala koyamba iwo kupita m’dzikoli chitengeleni udindo wa mtsogoleri wa dziko lino.

“Anthu akhoza kufuna kudziwa kuti ulendowu ndi wambiri yake yake kaamba koti aka ndikoyamba a Chakwera kupita m’dzikoli kuyambira pomwe adatenga udindo wa mtsogoleri wa dziko lino.

“Choncho ulendowu ukalimbikitsa ubale wa dziko la Malawi ndi dziko la China komaso kutsimikiziranso kugwirizana kwa chuma ndi malonda pakati pa mayiko awiriwa,” watelo undunawu mumchikalatacho.

Malingana ndi chikalatachi, a Chakwera akuyembekezeka kubwelera m’dziko muno Lolemba pa 3 July, 2023 ndipo ndege yomwe adzakwere ikuyembekezeka kudzatela pa bwalo la Kamuzu nthawi ya 13:35.

A Chakwera akupita mdziko la China ndi anthu angapo omwe chikalatachi sichinafotokoze kuti ndi angati koma chati anthuwa ndi nthumwi za makampani a m’dziko muno omwe akatenge nawo gawo pa chionetsero cha malonda.

Follow us on Twitter:

Advertisement