Akatswiri pa malimidwe alimbikitsa kuteteza nthaka ndi zachilengedwe

Advertisement

Akatswiri pa za malimidwe atsindika pa kufunikira koteteza nthaka kuti alimi azikolora chakudya chokwanira.

Mkulu oyendetsa polojekiti ya Adaptation Fund a Gilbert Kapunda ati kuguga kwa nthaka kuphatikizanso kusintha kwa nyengo kwakhudza kwambiri ntchito za ulimi mu dziko lino zomwe zapangitsa kuti alimi asamakolore zochuluka.

Polojekiti ya Adaptation Fund yomwe cholinga chake ndi kulimbikitsa kuteteza nthaka komanso zachilengedwe pothana ndi mavuto omwe akubwera kaamba kakusintha kwa nyengo ikuthandizira kubwezeletsa nthaka nchimake komanso kuteteza za chilengedwe zosiyanasiyana.

Poyankhula pa mwambo okhazikitsa ndondomeko ya kasamalilidwe komanso katetezedwe ka chilengedwe komanso nthaka m’boma la Balaka, a Kupunda anamema alimi kuti akhale patsogolo poteteza nthaka komanso zachilengedwe ndi cholinga choti azikhala ndi ulimi opindulitsa.

Iwo adatsindika kuti nthaka ya chonde ndi gwero la ulimi opindulitsa.

”Chaka ndi Chaka, zokolora zathu zikumka nacheperachepera kusiyanitsa ndi kale kaamba ka kukokoloka kwa nthaka ya chonde. Chotero, ndi kofunika ngati dziko kuti aliyese akhale patsogolo kulimbikitsa komanso kusamalira nthaka komanso zachilengedwe kuti tizitha kukolora chakudya chochuluka,” anatero a Kupunda.

Mkhalapampando wa ulangizi m’boma la Balaka a Mercy Chakoma anati kuguga kwa nthaka, ng’amba komanso kusefukira kwa madzi kwakhala kukukhudza kwambiri ulimi m’boma la Balaka ndipo wapempha alimi kuti azitsatira ndondomeko zonse zosamalira nthaka komanso kuteteza chilengedwe.

Iwo adalimbikitsaso alimi kuti azigwiritsa ntchito manyowa kuti zithandizire kubwezeletsa nthaka nchimake.

M’modzi mwa anthu omwe akupindula ndi polojekiti ya Adaptation Fund, a Julita Ntchetche, ati apindula kwambiri kudzera mu upangiri wa njira za makono za ulimi zomwe zathandizira kuti pakhomo pawo pakhale pa mwanaalirenji.

Kudzera mu polojekiti ya Adaptation Fund, alimi komanso anthu a mdera la mfumu yaikulu Amidu m’bola la Balaka akugwira ntchito zosiyanasiyana monga
kubzala mitengo, ulimi wa mbeu zosiyanasiyana komanso ziweto kuphatikizapo kukhala m’mgulu a banki yakumudzi, magulu omvera wailesi momwe amapeza ulangizi wa makono okhuzana ndi ulimi.

Polojekiti ya Adaptation Fund ikugwiridwa ndi chithandizo cha ndalama chochokera ku bungwe la World Food Programme (WFP).

Follow us on Twitter:

Advertisement