‘Ponya kaye K10,000 mami, onetsa lavu’ – mneneri Habakkuk watekesa pa intaneti

Advertisement

…akuti ku utumiki kwawo aziyimba nyimbo za hipapa, piyano

Aneneri ndi onse koma umanena uyo wakulasa mtima mosayang’anira maonekedwe, ndipo poti dzuwa salozerana, sizochitaso kukambirana kuti mneneri Habakkuk watenga mitima ya mazana mazana ya aMalawi. Timutche mneneri wa pa intaneti?

Masiku ano ukumati ukalowa m’masamba anchezo, mwa zinthu khumi zoyambilira kuziona, zisanu ndi ziwiri zikumatha kukhala zithuzi, makanema kapena tinkhani toduka mutu ta mneneri Habakkuk.

Koma kodi Habakkuk ndindani kwenikweni, amakhala kuti, komaso kodi ‘munthu wa Mulungu yu’ amapanga chiyani pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku?

Malingana ndi masamba a nchezo, Habakkuk ndi mneneri wa Mulungu yemwe anayambitsa utumiki wotchedwa Prophet Foundation ndipo mkuluyu amapezekela ku mpoto kwa dziko lino, m’boma la Rumphi.

Kwa pano sitinapeze kuti kwenikweni mneneriyu amapanga chiyani kuti apeze chakudya cha moyo wake wa tsiku ndi tsiku kupatula kutsogolera ‘nkhosa’ kuchipulotso monga mwa ntchito ya mneneri.

Chatsitsa dzaye kuti mneneri Habakkuk atchuke kuposa mmene zatchukira mbatata mchakuti ali ndililime lakuthwa lomwe likayankhula chinthu, mawu ake akumakhala achikoka ndipo akumatha kukusiya munthu kukamwa kuli yasaa, osavetsa.

Monga momwe zinaliri ndi msangulutsi Henry Gopani, Habakkuk naye akumati akafika pamalo aliwose, aliyese akumafunitsitsa kujambulitsa naye ndipo amuna osaugwira mtima atha kuyamba kuchita nsanje za pusi kaamba koti mkuluyu wazulaso mitima ya azimayi.

Mwezi uno, Habakkuk anagwedeza kwambiri masamba a nchezo kamba ka zomwe anayankhulana ndi mzimayi wina yemwe mwa nthabwala anamuyimbira foni mtumikiyu kumuuza kuti wagwa naye mchikondi, akumufuna banja.

Anthu omwe amvera zomwe a Habakkuk anamuyankha mzimayi othothoka sidzeyu akumagwa ndiphwete kwinaku akupukusa mutu, kudzifusa kuti kodi watani mtumiki wa Mulungu kufika mlingo uwu.

“Tsono ndi we wakuti amene ukufuna ukhale swita wanga, ndiwe wakuti ukufuna ndikukwatile kuti tizitumikira tonse ntchito ya ambuye, ndiwe wa kuti mami? Udzabwera liti? Ine ndimakhala ku Rumphi pa boma. Ngati umandikondadi ubwere ku Rumphi pa boma mami, uzaone pomwe ndimakhala, ndizakuonetsa kwa azibusa anga kuti uyuyu akufuna ndimukwatile.

“Utumize ndalama K10,000 pa Airtel money yangayo, ndikhulupilire kuti uyuyu akufuna ndimukwatiledi. Sindikukupasa chilango ayi, utumize owonetse lavu, utumize mawa kuti ndivomeleze kuti uyu ali siliyasi,” anatelo a Habakkuk pomuyankha mkazi yemwe anawafusira banjayo.

Munthu ukamva zina mwa nkhani za mkuluyu zikumavuta kumvetsa kuti kodi m’mutu mwake mumakoka bwino bwino kapena mawaya ena mu ubongo wake anasempha?

Mwachitsanzo, mumakilipi ena, Habakkuk anauza anthu kuti ku utumiki wawo wa Prophetic Foundation, ayamba kumayimba nyimbo zosiyanasiyana kuphatikizapo za hipapa komaso piyano.

“Nyimbo zimene tiziyimba pa Prophetic Foundation ndi lege koma yomutamanda Mulungu, ngakhale si lege koma zizikhala zomutamanda Mulungu, kaya ndi nyimbo za malapu (rap), kaya ndi hipapa (hip hop), kaya ndi nyimbo za piyano, koma zikhale zomulemekeza ambuye,” watelo Habakkuk.

China chodzetsa tsemwe mchakuti mneneri Habakkuk akumalankhula mosapsatira kuti ntchito yopemphera ndiyovuta kwambiri ndipo anthu akuyenera kumapeleka kaye dipo kwa iwo kuti apempheleledwe.

Mkuluyu wati nthawi zina kuti munthu ulandire dalitso lako umayenera kuti upeleke kanganyase kwa mtumikiyo kuti akamakupemphelera azikhala ndimphamvu.

“Kuti chozizwa chikuchitikire ukuyenera upeleke nsembe zinthu mzako zina. Chozizwa china chimafuna kuti munthu uwombole ndi ndalama. Kwa papa sitimapeleka wambawamba. K30,000 yoyimira tate, mwana ndi mzimu woyera. Mukatumiza ine ndikupemphelerani,” Habakkuk anauza munthu wina yemwe amafuna pemphero.

Ngakhale zomwe akumayankhula nkuluyu zili zoduka mutu, koma makilipi ake achulukana ngati mchenga pa masamba a nchezo ndipo anthu ochuluka zikuwasangalatsa, enaso akuti zikumawachotsa nkhawa zosiyanasiyana malingana ndi kuvuta kwa chilembwe pa mpanje pano.

Ngakhale zili choncho, anthu ena ati mpofunika kufuza bwino bwino umoyo wa mkuluyu ponena kuti mwina mkuluyu ndiofunika kum’tengera ku chipatala cha zaubongo kuti akawunikidwe ngati sakudwala matenda amubongo.

“Mkulu uyu watchukayu, prophet Habakkuk mentally ngwa bwino bwino? Kulipotu making fun of an individual who needs some mental help. Komanso, omwe akumujambula ma videos, mkuluyi akumachita mwa chifuniro chake kapena ai?

“Ali ndi abale ake? Ngati alipo, akamaona ndi kumva tima clip tili mbwee iti amati chani? Si abambo kapena agogo a munthu wina wake mkulu ameneyu? Koma ndiye mwatchukatu. Duzi-duzi ndi mbatata!” Watelo munthu wina pa fesibuku.

Follow us on Twitter:

Advertisement