Chipani cha UDF chikufuna kudzalowa m’boma mu 2025

Advertisement

Chipani cha United Democratic Front (UDF) Lamulungu chidakondwelera kuti chatha zaka 30 chiyambireni chipanichi ndipo chapempha ochitsatira kuti asamanyozane pofuna kuti UDF idzalowenso mu boma pachisankho cha chaka cha 2025.

Poyankhula pa bwalo la St Augustine 3 mu Boma la Mangochi, mtsogoleri wachipani cha UDF Mai Lilien Patel adati chipanichi ndichomwe chidayambitsa demokalase mdziko muno ndipo adathokoza anthu omwe adachiyambitsa monga mtsogoleri wakale wadziko lino Dr Bakili Muluzi, a Brown Mpinganjira, Malemu Aleke Banda, Harry Thomson, a James Makhumula, Dr Dumbo Lemani kungotchulapo ochepa.

Mai Patel adalangidza anthu okonda chipanichi kuti asamanyozane komanso kuchitilana kaduka popeIza chipanichi ndicha munthu wina aliyense.

Pamenepa iwo adapemphanso anthu osatira chipani cha UDF kuti asamaletse anthu omwe akufuna kulowa chipanichi kuti alowe komanso omwe adatuluka muchipanichi ngati akufuna kubwelera athe kubwelera.

Mai Patel adatinso iwo sakapikitsana nawo paudindo wautsogoleri wachipanichi pamsokhano wake waukulu omwe uchitike chaka chino ndipo adapempha aliyense yemwe akufuna kukapikitsana paudindo uliwonse kuti abwere poyera.

“Pali anthu ena muchipanichi omwe amadzitenga ngati ndiwopambana kuposa anzawo koma chomwe angadziwe ndichoti malamulo achipani cha UDF samalola kunyozana komanso ndikufuna anthu adziwe kuti chipani chathu ndichomwe chidayambitsa demokalase kuno ku Malawi,” adatero Mai Lillien Patel.

Poyankhulanso, yemwe adali mlendo wapadera pansokhanowo Atupele Muluzi adati chomwe akufuna ndichoti alimbikitse chipanichi kuti chikhale champhamvu mdzigawo zonse zadziko lino.

A Muluzi adati chipani cha UDF ndichokhulupilira demokalase choncho aliyense akhoza kukapikitsana nawo pampando wina uliwonse ku convention.

Pamenepa iye adati ali okonzeka kukapikisana nawo pachisankho pamsonkhano wake waukulu omwe udzachitike chaka chino.

Ena mwa anthu odziwika bwino omwe adalinawo pamsonkhanowo ndi monga, mtsogoleri wachipani mchigawo chammawa a Hashim Banda, Dr Yusuf Mwawa, a Clement Sitambuli, a Samson Msosa, Wachiwiri kwa Speaker wakunyumba yamalamulo Aisha Mambo Adams, Mtsungi chuma wankulu wachipani cha UDF a Nedson Poya ndi ena ambiri.

Follow us on Twitter:

Advertisement