Asilikali awiri omwe anasowa dzulo apezeka

Advertisement

Asilikali omwe anasowa dzulo ku Mulanje pamene boti lomwe anakwera linakokoloka ndi madzi apezeka.

Nduna yowona za Chitetezo a Harry Mkandawire ati awiriwa agona mu mtengo ndipo anthu omwe ali kumeneko atsimikiza kuti ayankhulana nao.

Malingana ndi nduna ya za ma boma a Richard Chimwendo Banda omwe anali pa Mkando m’boma la Mulanje, dzulo asilikali atatu a pamadzi ananyamuka pa bwato ndicholinga chofuna kukapulumutsa anthu ena omwe anali pamwamba pa malo othilira mafuta agalimoto.

Malipoti akusonyeza kuti asilikaliwa ali mkati mwa ulendo wawo, bwato lomwe anakwelaro linazima ndipo linayamba kukokoloka ndi madzi aphanvu omwe ali mdelari.

Bwatoli linakagunda mtengo zomwe zinapangitsa kuti litembenuzike ndipo munthu wamba mmodzi komaso asilikali awili ndi omwe anakwanitsa kuwolokera ku mtunda koma asilikali atatu anasowa.

Patatha ka nthawi kochepa, a Chimwendo Banda anauza anthu kuti msilikali mmodzi mwa atatu omwe anasowawa wapezeka ali mu mtengo wina.

Mulanje ndi Boma limodzi lomwe lakhudzidwa ndi madzi osefukira komanso namondwe yemwe akutchedwa Freddy.

Follow us on Twitter: https://twitter.com/Malawi24

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.