Khansala wabanduka atagulitsa geledala yaboma

Advertisement
Malawi24.com

Apolisi m’boma la Chiradzulu akhazikitsa kafukufuku osaka a Douglas Mkwezalamba omwe ndi a khansala a wadi ya Mwanje kaamba kogulitsa geledala yaboma pamtengo wa K3.5 miliyoni.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi mneneli wapolisi ya Chiradzulu a Cosmas Kagulo omwe ati apolisi anatsinidwa khutu kuti Mkwezalamba akugulitsa geledala ya boma kwa nzika ina yaku Tanzania.

Potsatira kutsinidwa khutuku, apolisi anathamangira pamalo omwe geledalayi imasungidwa pomwe akuti yakhalapo nthawi yaitali osagwilitsidwa ntchito kaamba koti inaonongeka.

Atafika pa malo pomwe panali geledalayi, apolisi anapeza anthu ena akumasula zitsulo za geledalayi ndikumakazikweza mgalimoto ina, ndipo pofusafusa, zinadziwika kuti geledalayi ndiyaboma pansi paunduna wa zamtengatenga ndi mtokoma.

Apa apolisiwa anamanga a Verian Adams Shuli aku Tanzania omwe akuti ndiomwe amafuna kugura geledalayi komanso anamanga a William Katete omwe amathandizira ntchito zina zogulitsira makinawa.

Omangidwawa ndi omwe anaulura kuti makinawo akugulitsidwa ndi a khansala a Mkwezalamba ndipo zadziwika kuti pa nthawiyi, a khansalawa anali atalandira kale ndalama yokwana K1,845,000 pa K3.5 miliyoni yomwe anatchaja ndipo akuti ndalamayi anaitumiza kwa a Mkwezalamba kudzera pa Airtel money.

Atatsinidwa khutu kuti akufunidwa ndi apolisi, khansala Mkwezalamba anangoti phazi thandize ndipo komwe ali pakadali pano sikunadziwike ndipo a polisi ati ayamba ntchito yosaka khansalayu.

Malipoti akusonyeza kuti, khansalayu anapeza mpata ofuna kugulitsa geledealayi kaamba koti yakhala nthawi yaitali osagwilitsidwa ntchito ndizikuoneka kuti khansalayu amaganiza kuti boma silikukumbukiraso za makinawa.

Follow us on Twitter:

Advertisement