Osamadikula mu tchalichi mukamavina — Bishopu wachenjeza a Katolika

Advertisement

A Katolika awachenjeza kuti asamadikule mu tchalichi chifukwa kavinidwe kotero kangathe kupangitsa kuti akhristu anzawo achimwe.

Bishopu wa ku Ndola a Benjamin Phiri ati ndi okhudzidwa ndi m’mene anthu amavinila mu tchalichi pa nthawi ya Misa popeza ena amadikula kwambiri.

Malingana ndi mkulu wa ansembeyu yemwe mawu ake asindikizidwa ndi nyuzipepala ya Ku Zambia ya Daily, kuvina kwa mu tchalichi simbali imodzi yosangalatsa anthu ndiye kukuyenela kuzikhala kosiyana ndi mavinidwe a ku mabala kapena malo azisangalalo.

“Osamadikula kwambiri chifukwa mukamatero akhristu ena azikhala ndi maganizo olakwika, osayenera mu tchalichi,” anatero Bambo Phiri.

Iwo anapempha kuti akhristu akufunika azikhala oziletsa okha kuti mavinidwe a mu tchalichi azikhala olemekeza Mulungu ndipo asamafanane ndi a mu malo azisangalalo.

Follow us on Twitter:

Advertisement