Chakumwa nacho Chakwera


Kampani yofulula mowa ya Castel yalengeza kuti mitengo ya zakumwa zawo zoiwalitsa mavuto amene dziko lino likukumana nawo azikweza. Ati kuyambila mawa, mowa ukhala okwelelako mtengo.

Malinga ndi chikalata chomwe kampaniyi yatulutsa, mitengo ya mowa ikukwela kamba ka kukwela mitengo ya zinthu mu dziko muno.

“Takakamizika kukweza mitengo kamba ka kusintha kwa mitengo mu dziko lino,” atelo a Castel.

Mwa zina iwo anenapo kuti kusowa kwa ndalama za mayiko a kunja, forex, ndinso kugwetsedwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha ndiko kwapangitsa kuti aunikile bwino lomwe mitengo yawo.

“Pamene Kwacha inagwa, malonda athu anakhuzika moti tinaonjezela 27% pa ndalama zimene timafuna pa Mwezi,” alengeza choncho a Castel.

Pa mtengo wa tsopano, mowa wa Kuchekuche uzigulitsidwa pa mtengo wa K700 ndi Kampani ya Castel pomwe mowa wa Premier Brandy uzigulitsidwa K10, 000.

Follow us on Twitter: