Chakwera atukwanidwa ku Blantyre

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera lolemba sabata ino anawowozedwa komaso kutukwanidwa ndi anthu mumzinda wa Blantyre.

Izi ndimalinga ndi kanema yemwe tsamba lino lawona yemwenso anthu akugawana m’masamba a mchezo yemwe akuonetsa anthu akutukwana mtsogoleri wa dzikoyu pomwe amachoka kokagwira ntchito ya boma ku Thyolo.

Patsikuli a Chakwera anapita kokayendera mbewu m’minda mwa anthu ena ku Thyolo ndipo pobwerako, anthu ena anayamba kumukuwiza komanso kumutukwana mtsogoleriyu pomwe amadutsa mu Limbe.

Ena mwa mawu omwe akuveka chapansipansi mu kanemayi ndiodandaula kuti zinthu zikukwera mitengo tsiku ndi tsiku ndipo ena mwa anthuwo amakuwa mkumanena kuti “achoke, achoke”.

Koma nkhaniyi yakwiyitsa mmodzi mwa anthu odziwika bwino pa tsamba la facebook a Onjezani Kenani omwe ati mchitidwewu ndiosakhala bwino ndipo ati ukuyenera utheletu mdziko muno.

A Kenani ati pulezidenti ndi tate wa dziko ndipo akuyenera kulandira ulemu woyenelera nthawi zonse ndipo ati ngati pali kusemphana, ndibwino kupeza njira zina zothandizira kuti mabvuto omwe tikudutsamo athe osati kumutukwana.

“Kutukwana a Pulezidenti, ngati zomwe zachitika dzulo ku Blantyre pomwe magalimoto awo amadutsa – molingana ndi m’mene vidiyo ina ikuwonetsera – ndi chinthu cholakwika kwambiri. Tiyeni titsutsane nawo mwaulemu pazimene sizikutisangalatsa, koma kuwatukwana sichinthu chabwino.

“Ngati zomwe akuchita sitikugwirizana nazo, nthawi yathu yodzawawonetsera kusakondwa kwathu idzabwera tsiku lovota. Koma panthawi ino tiwapatse ulemu monga mtsogoleri amene tinamusankha kuti ayendetse dziko lino,” atelo a Kenani.