Chakwera atukwanidwa ku Blantyre

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera lolemba sabata ino anawowozedwa komaso kutukwanidwa ndi anthu mumzinda wa Blantyre.

Izi ndimalinga ndi kanema yemwe tsamba lino lawona yemwenso anthu akugawana m’masamba a mchezo yemwe akuonetsa anthu akutukwana mtsogoleri wa dzikoyu pomwe amachoka kokagwira ntchito ya boma ku Thyolo.

Patsikuli a Chakwera anapita kokayendera mbewu m’minda mwa anthu ena ku Thyolo ndipo pobwerako, anthu ena anayamba kumukuwiza komanso kumutukwana mtsogoleriyu pomwe amadutsa mu Limbe.

Ena mwa mawu omwe akuveka chapansipansi mu kanemayi ndiodandaula kuti zinthu zikukwera mitengo tsiku ndi tsiku ndipo ena mwa anthuwo amakuwa mkumanena kuti “achoke, achoke”.

Koma nkhaniyi yakwiyitsa mmodzi mwa anthu odziwika bwino pa tsamba la facebook a Onjezani Kenani omwe ati mchitidwewu ndiosakhala bwino ndipo ati ukuyenera utheletu mdziko muno.

A Kenani ati pulezidenti ndi tate wa dziko ndipo akuyenera kulandira ulemu woyenelera nthawi zonse ndipo ati ngati pali kusemphana, ndibwino kupeza njira zina zothandizira kuti mabvuto omwe tikudutsamo athe osati kumutukwana.

“Kutukwana a Pulezidenti, ngati zomwe zachitika dzulo ku Blantyre pomwe magalimoto awo amadutsa – molingana ndi m’mene vidiyo ina ikuwonetsera – ndi chinthu cholakwika kwambiri. Tiyeni titsutsane nawo mwaulemu pazimene sizikutisangalatsa, koma kuwatukwana sichinthu chabwino.

“Ngati zomwe akuchita sitikugwirizana nazo, nthawi yathu yodzawawonetsera kusakondwa kwathu idzabwera tsiku lovota. Koma panthawi ino tiwapatse ulemu monga mtsogoleri amene tinamusankha kuti ayendetse dziko lino,” atelo a Kenani.

Advertisement

6 Comments

  1. Utsogoleri udzitumikira anthu ake mopanda tsankho, ndiye umakondwetsa anthu.Iwowo zimene akuchita ndizosemphana ndi zimene amanena pa nthawi yokopa anthu kuti awavotere. Anthutu chilowereni mkulu ameneyi akuvutika kwambiri komanso palibe cha nzeru chimene akupanga kuno ku South. Pajatu ankadana ndi Lomwe belt pano kuli chewa belt, ndiye ubwinowo uli pati. Tsankho amadana nawo lija pano ndiye linyanya mu ustogoleri wawowu, Munthu zowona mukatenga apongozi ako ndi mwana yemwe kuti azipwepweta ndalama za a Malawi ife. Pomwe fertilizer anthu avutika osampeza okwanira chaka chino.
    Ndiye inu a Kenani kaya mwadya chani, kapena mwafika kale ku Kenani kuja amnzanthu?

  2. Amalawi amafika potopa, akatopa amalankhula, ichichi nde muchikhazikitse mmitu mwanumo. Do you know why people act on these issues? We Malawian sitipereka report. Mukanamapereka ma report on why things are getting expensive like this bwezi tikunvetsetsa. But u speak out anthu akakuyalutsan, give us a report, when we argue, u will remind us about the report you presented. Zinthu zikukwera not because Chakwera what’s things to be like that, but something uncontrollable by him is happening. So let us know and let other expats guide. #my_malawi

    1. I hope these people have something to do because even if a new president comes if ur job is to steal in limbe then you will keep on complaining until ur death

  3. A muchita bwino, anthu ku Thyolo komweko agula dothi kumawanamiza kuti ndi fertilizer, nde akukayendera mbewu zake ziti, walephera kuwasapota a Malawi paulimi, now akuti akuyendera minda, akukaonamo chani. Afunse anthu mbuyomu, minda imene Dr Kamuzu Banda amayendera imakha itathandizidwa kudzera mmakarabu a admarc ngati boma pofuna kulimbikitsa ulimi wamakono komanso food security. Don’t take Malawians for a ride. Mulungu adzakulangani.

  4. I think people have tired…or kukambirana sikikukuthekanso

Comments are closed.