‘Tulani pansi’ – Dan Lu wauza Chakwera

Advertisement

Katswiri oyimba nyimbo zachamba cha afro pop, Dan Lufani, yemwe amadziwika ndi dzina loti Dan Lu wauza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti alephera kulamulira ndipo atule pansi udindo.

Izi ndi malingana ndi nyimbo yatsopano yomwe Dan Lu watulutsa lachitatu pa 23 March yomwe mutu wake waipatsa kuti ‘Tulani pansi’ ndipo ikulamula kuti mtsogoleri wa dziko linoyu atule pansi udindo wake.

Katswiriyu yemwe adaimbaposo nyimbo zingapo zandale kuphatikizapo nyimbo yotchuka kwambiri ya ‘Lozani Zanu’, wati mtsogoleri wa dziko lino walephera kukwanilitsa zomwe ananena kuti adzachita akadzalowa m’boma ndipo atule pansi udindo.

Tulani pansi udindo, tulani x4

Mwatilephera, tulani

Tulani pansi udindo, tulani

Mwatikanika, tulani

Tulani pansi udindo, tulani,” ikumatero kolasi ya nyimboyi.

Mu m’nyimboyi, Dan Lu waikamo mau a Chakwera omwe anayankhula nthawi yokopa anthu ndipo anati adzatula pansi udindo wake ngati angadzalephere kusintha zinthu mu zaka ziwiri zoyambilira zaulamuliro wake ndipo oyimbayu wati mtsogoleriyu achite zomwe adanenazi.

Siine koma pakamwa panu n’pomwe padanena

Mwina muzati mwanayu ndiwamwano, amangotizonda

Kapena watumidwa, ayi munanena nokha

Nsanje to Chitipa, ikudziwa kuti munanena nokha,” yatero vesi yoyamba ya nyimboyi.

Oyimbayu watiso anthu ambiri m’mamidzi ndi mmatauni akulira kaamba ka mavuto adzaoneni omwe azinga dziko lino ndipo wati anthu.

“Kulephera kugula shuga, kusamba opanda sopo, tikudya zosipa mpaka tayambapo kuvala dzigamba,” ikutero nyimboyi.

Dan Lu wadandaulaso kuti pali tsankho pankhani yolemba anthu ntchito kaamba koti ntchito zambiri zikupelekedwa kwa achibale azitsogoleri a dziko lino komaso makontalakiti akupelekedwa kwa anthu omwe ali ndi achibale m’boma.

Mbali ina yavesi yomaliza ya nyimboyi, Dan Lu wati:

Feteleza uja wakanika kutsika

Nkhani ya mapasipoti, ntchito nde zikusowa

Munanena nokha ndipakamwa panu

Sikuti mwina munatumidwa, koma munanena nokha.”

Pakadali pano anthu ambiri makamaka omwe ayikira ndemanga patsamba la fesibuku la katwiriyu, ati ayilandira bwino nyimboyi pomwe ena ati Dan Lu wayimba nyimboyi kaamba koti chipani cha DPP sichili m’boma.

Pamene chipani cha DPP chinkalamulira, Dan Lu ankatulutsa zochemelera chipanicho ndipo imodzi mwa nyimbozi ndi Lozani Zanu.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.