Utsogoleri wa Boma la Tonse ndi wofooka – atero mabishopu

Advertisement

Mabishopu a Chikatolika adzudzula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti akumachedwa kumanga mfundo maka pa nkhani yothana ndi katangale ngakhale kuti ali ndi mphamvu zowalora kuchita zinthu mu nthawi yake.

Mabishopuwa anena izi mu kalata yomwe atulutsa lero ndipo yasayinidwa ndi mabishopu asanu ndi awiri a mdziko lino.

Mu kalatayi, ma bishopu ati boma la a Chakwera linapatsidwa mphamvu  koma likumachedwa kuchita zinthu makamaka pa nkhani za mchitidwe wa katangale okhudzana ndi nduna komanso alangizi a mtsogoleri wa dziko lino.

“Tikukhulupirira kuti, President amene adaachita kampeni potsamira pa Mfundo yolimbana ndi katangale ndiponso amene adaalonjeza kuti athana ndi vutoli, sayenera kuikira kumbuyo nduna ndi omuthandizira ake omwe akuganiziridwa kuti adatenga nawo mbali pa nkhani yokhudza mchitidwewu, makamaka pamene pali umboni wokwanira,” chikalatachi chatero.

Mabishopu anenanso kuti ndi okhudzidwa ndi malipoti omwe akuonetsa kuti mabungwe aboma, maunduna, madipatimenti ndi nthambi zina zaboma zidaima chifukwa akudikira chilolezo kuchokera ku Ofesi ya President ndi Cabinet (OPC) ndipo nthawi zina, kudikiraku kumatenga miyezi mpaka isanu.

“M’malo moti OPC ikhale chitsanzo cha utsogoleri wabwino wotumikira anthu m’nthawi yake, yasanduka Ofesi imene ikulephera kukwaniritsa ntchito yake yotumikira anthu. Kagwiridwe ka ntchito ndipo kuthekera ndi kuyenerezeka kwa anthu akuluakulu a mu Ofesi imeneyi, kuyenera kuwunikiridwanso ndipo pachitike kanthu mwamsanga,” ma Bishop atero.

Aepiskopi a Mpingo Wakatolika atinso ndi okhumudwa pakumva kuti chuma cha dziko la Malawi chikuwonongedwa ndi alendo mogwirizana ndi andale ndi antchito a m’boma okonda katangale.

Iwo ati nkhani za katangale zomwe zidaululika posachedwazi zitha kupereka mwai ku dziko la Malawi kuti liwonetse poyera kuti nkhondo yolimbana ndi katangale siyapakamwa chabe, koma ndi nkhondo yeniyeni yofuna kuthana ndi katangale m’dziko lino.

Iwo adzudzulanso ndale zongofuna kukondweretsana popatsana maudindo mokondera makamaka pa kasankhidwe ka mabwana akuluakulu m’mabungwe aboma.

“Ife tikuganiza kuti, pofuna kuthetsa mavutowa mwamsanga, pakusoweka kukhala ndi utsogoleri wotha kulowererapo pamene zinthu zikulakwika pofuna kupititsa patsogolo ulemerero, chilungamo ndi kufunika kotsata lamulo nthawi zonse.

“Tikudziwa kuti mabungwe amenewa (parastatals), amatolera ndalama zambiri zimene sizigwiritsidwa ntchito podzera m’ndondomeko za ndalama zogwiritsidwa ntchito ndi Boma. Izi zimachititsa kuti mabungwewa azigwiritsa ntchito ndalamazo mwachisawawa ndi mopanda kalondolondo. Izi zimachitika dero pofuna kuti ndalama ndi zinthu zina zaboma zikwaniritse zolinga za anthu andale ndi anthu ena ofuna kudzilemeretsa.

“Mabungwe amenewa akuyenera kumagwira ntchito moima paokha ndi mosabisa kanthu pamaso pa Amalawi. Mwatsoka ilo, kulowerera kumene kumachitika ndi Ofesi ya President ndi Cabinet pakayendetsedwe ka mabungwewa, ndi chizindikiro chooneka cha kuchita zinthu mosalabadira lamulo,” kalatayi yatero.

Apa ma Bishop apempha boma la a Chakwera kuti lichitepo kanthu powonetsa utsogoleri wabwino.

 

Advertisement