Kalindo wasambwadza boma

Advertisement

…waitanitsa ma demo sabata yamawa…

M’modzi mwa anthu odziwika bwino pa ndale omweso ndi membala wa chipani cha UTM, a Bon Kalindo, adzudzula atsogoleri a boma kaamba kolephera kuyendetsa bwino dziko lino.

A Kalindo omwe amadziwikaso ndi dzina la Winiko amayankhula izi pomwe amacheza ndi wailesi ya kanema ya Rainbow Lachinayi ndipo anati ndiokhumudwa kwambiri kaamba koti zambiri zomwe mgwirizano wa Tonse unalonjeza nthawi ya kampeni sizikuchitika.

Iwo anati alephera kudzigwira kaamba kakukwera mitengo kwa zinthu m’dziko muno zomwe anati ndichisonyezo kuti zinthu sizili bwino ndipo aloza chala mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi wachiwili wawo Saulos Chilima.

Mkuluyu watiso ziphuphu ndi katangale zomwe akuchita akuluakulu aboma la Tonse ndi zomwe zapangitsaso kuti mavuto afike pamponda chimera mdziko muno.

A Kalindo ati ndizokhumudwitsa kuti a Chakwera akumauza anthu kuti apilire pamavuto adzaoneni omwe ali mdziko muno pamene iwowo tsiku ndi tsiku akudya zatswayitswayi lunyumba kwawo.

“Funso mkumati kodi iwowo akupilira, akudikilira? Kodi ndizoona kuti munthu azidya nsima nde aziwauza anzake kuti dikilirani pamene iyeyo akudya, pali nzeru pamenepo? Atsogoleri amenewawa ndi amene anakhulupililidwa kwambiri koma akukhumudwitsaso anthu kwambiri,” watelo Kalindo

Kalindo wadzudzulaso a Chilima chifukwa chongokhala chete osayankhulapo pamene zinthu zikulakwika ndipo wati akuyenera kumapeleka chilimbikitso kwa a Malawi ponena kuti anthu ambiri anavotera mgwirizano wa Tonse chifukwa cha a Chilima.

“Anthu anavotela bomali chifukwa cha a Chilima ndipo onsewa amafuna kusintha koma a Chilima afatsa kwambiri. A Chilima akuyenera atuluke chifukwa kutsogoloku akadzawauzaso aMalawi kuti mavutowa ankawaona, anthu sadzawakhulupiliraso­.

“Chilima paja amatitu ndioganiza bho, nde tikuti abwere azawayankhule aMalawi. Tikuyankhula pano Achinyamata kuphatikiza a UTM akuvutikatu,, alibe chochita nde tikuti abwere atiuze chifukwa chimene feteleza amkati azatchipa uja wakwera mtengo kwambiri,” anaonjezera choncho a Kalindo.

Mkuluyu anati ndiodabwa kuti a Chakwera ndi akuluakulu ena aboma akhala akutoza DPP kuti m’boma sanapezemo kanthu ndipo ati ichi chimangokhala chiyankhulo cha anthu andale ponena kuti zinthu anazipeza koma akuziononga okha.

Iwo apepesa kumtundu wa aMalawi ati kaamba koti ankaima mmisonkhano kumanena kuti kudzakhala ntchito kwa achinyamata, feteleza adzatsika mtengo zomwe akuti pano zonsezo ndi maloto achumba.

 

Apa a Kalindo anati: “Tinkayima mmisonkhano kuwaza anthu kuti ntchito zikubwera, feteleza otchipa adzakhalapo koma ndine okhumudwa chifukwa zonse zomwe timawauza anthu sizinachitike,”

Pakadali pano malingana ndi chikalata chomwe tsamba lino laona, a Kalindo ayitanitsa zionetsero zomwe zichitike m’mizinda yonse yadziko lino koma zichitika masiku osiyanasiyana ndipo zikuyamba lachisanu sabata lamawa mumzinda wa Blantyre.

Advertisement

One Comment

  1. Winiko akupanga zokomela ife amphawi ndipo I will sport him coz he do something gd

Comments are closed.