Kampani yopanga shuga ku Salima yatsekedwa kaamba ka Covid-19

Advertisement

Unduna wa zaumoyo mogwirizana ndi komiti ya mtsogoleri wadziko yotsogolera ntchito yolimbana ndi covid-19, yatseka kampani yopanga shuga m’boma la Salima potsatira imfa yaogwira ntchito mmodzi ochokera mdziko la India yemwe anapezeka ndi matendawa.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi nduna ya zaumoyo mai Khumbize Kandodo Chiponda omwe amayankhula Lachiwiri podziwitsa anthu za mmene dziko lino likuchitira pantchito yolimbana ndi mlili wa covid-19.

Iwo ati undunawu komaso komitiyi, analandira uthenga oti ku kampaniyi kwabwera anthu ochokera mdziko la India komaso Pakistan komwe mlili wa covid-19 wavuta kwambiri ndipo ati anatapita kuti akatsimikize zankhaniyi komaso akawayeze anthuwo.

Kandodo Chiponda

A Kandodo Chiponda ati atawayeza, anthu 22 mwa anthu 60 omwe abwera posachedwapa kuchokera ku India ndi ku Pakistan, apezeka ndi matendawa ndipo munthu mmodzi wamwalira Lolemba zomwe ati zinabweretsa chiganizo chotseka kampaniyi.

Iwo ati kuyisiya kampaniyi kuti ipitilize ntchito zake kumaika pachiopsezo ogwira ntchito ena omwe alibe kachirombo ka corona komaso anthu okhala m’mbali mwa zomwe ati zimaika miyoyo ya anthu kukampaniyi pa chiopsezo.

“Nkhani yokhudza kampani yopanga shuga ku Salima, ndizoonadi kuti kumeneku kwapezeka mzika 22 za mdziko la India komaso Pakistan zomwe zikudwala covid-19 ndipo mmodzi watisiya lolemba pomwe anabwera naye ku Kamuzu Central.

“Choncho pano tayamba tatseka kaye kampaniyi, kalata yake tawatumizira lero lachiwiri. Izi tachita ndicholinga chofuna kuteteza anthu ozungulira kampaniyi komaso ogwira ntchito ena kuti pasakhale kupatsirana matendawa,” atelo a Chiponda.

Iwo ati pakadali pano ayamba ntchito yoyeza anthu onse ogwira ntchito kukampaniyi kuphatikizapo onse omwe amakhala mozungulira kampani yopanga shugayi.

Apa ndunayi yati kampaniyi izatsekulidwaso onse ogwira ntchito ku kampaniyi omwe akudwala matenda a covid-19 akadzachira ndi cholinga chofuna kuteteza anthu ena omwe mliliwu sunawagwire ku kampaniku.

Advertisement