Potsatira kuchotsedwa ntchito kwa makomishonala awiri a bungwe loyendetsa chisankho la MEC, chipani chotsutsa boma cha DPP chati chipita kukhothi kukapempha kuti khothi lilamule kuti chisankho chachibwereza cha chaka chatha chinali chosayenera.
Nkhaniyi ikubwera pomwe boma kudzera kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera Lachiwiri lapitali achotsa pa ntchito ma komishonala a bungwe la MEC, a Jean Mathanga komanso a Linda Kunje.
Mlembi wa mkulu wa boma a Zangazanga Chikhosi anati awiriwa achotsedwa kaamba koti khothi lalikulu mdziko muno chaka chatha pa 8 May linawapeza kuti sanayendetse bwino chisankho chapatatu cha 2019.
Malingana ndi boma, kuwasiya awiriwa kuti akhalebe makomishonala a bungwe la MEC ndikulakwira gawo 75 ndime yachitatu ya malamulo adziko lino yomwe imakamba za kuchotsedwa nthito kwa komishonala yemwe sakuyenera kukhala komishanala.
Koma patangotha maola ochepa boma litabwera poyera ndikunena za kuchotsedwa kwa awiriwa, chipani chotsutsa boma cha DPP nacho chabwera ndimoto pomwe chati kuchotsedwa kwa a Kunje ndi a Mathanga nkosayenera.
Chikalata chomwe DPP yatulutsa chati zomwe achita a Chakwera zikutanthauza kuti kuchokera pomwe a Kunje ndi a Mathanga anasankhidwa kukhala makomishonala a MEC, zisankho zonse zomwe zachitika mdziko muno zinali zosayenera choncho pachitike chisankho china.
Apa chipanichi chati a Chakwera sakuyeneraso kukhala mtsogoleri wa dziko lino kaamba koti chisankho chomwe anapambana chaka chatha, chinayendetsedwa ndi a Kunje komaso a Mathanga omwe lero achotsedwa ponena kuti anali osayenera.
“Kubweza ganizo losankha makomishonala awiriwa, pompopompo kwapangitsa kuti ziganizo zonse zomwe bungwe la MEC lakhala likupanga kuyambira pa 7 June, 2020 kukhale koyenera mmalamulo.
“Democratic Progressive Party (DPP) ikuuza Dr Lazarus Chakwera kuti mwansanga nsanga achoke mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko. Iwo asakhaleso mtsogoleri wa dziko lino kaamba koti anasankhidwa pa chisankho chomwe chinayendetsedwa ndi bungwe lomwe linali losavomelezeka mmalamulo adziko lino,” yatelo DPP.
Pakadali pano bungwe la MEC lalengeza kuti lasiya kaye kugwira ntchito kaamba koti malamulo a dziko lino samalora kuti bungweli lipitilize kugwira ntchito pomwe makomishonala ena palibepo.
Mumchikalata chomwe MEC yatulutsa chati malamulo amati makomishonala abungweli amayenera akhalepo asanu ndi mmodzi nthawi zonse ndipo ati zatelemu bungweli lidzayambaso kugwira ntchito makomishonala olowa mmalo mwa awiriwa akadzasankhidwaso.
Nkhaniyi ikubwera pomwe posachedwapa mlangizi wa boma pankhani za malamulo Dr Chikosa Sulungwe analangiza boma kuti lisawachotse ntchito awiriwa ponena kuti sakuona vuto lililose kuwasiya kuti apitilizebe ntchito yawo