Tsiku lofika mapepala oponyera voti lasintha


Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lalengeza kuti pali kusintha patsiku lomwe ma pepala oponyela voti pachisankho chapadela afikile mdziko muno kuchokera ku Dubai komwe akupangidwa.

Izi ndimalinga ndi mneneri wa MEC a Sangwani Mwafulirwa omwe ati mapepalawa afika mdziko muno Lamulungu pa 21 March osatiso pa 25 March monga momwe zinalili poyamba ati kaamba kavuto la mayendedwe.

A Mwafulirwa ati bungweli limasakasa ndege yomwe ingazabweretse ma pepalawa pa 26 March ndipo ati zapezeka kuti patsikuli palibe ndege iliyose yomwe ikuzabwera Ku Malawi kuno zomwe zawapangitsa kuti asinthe tsiku lobwera ma pepalawa.

Mneneriyu wati mmalo mwake ndege yomwe bungweli lapeza ndiyobwera mdziko muno pa 21 March, 2021 ndipo ati magulu onse okhudzidwa pa chisankho chapaderachi adziwe zakusinthaku.

“Tinawapempha amzathu omwe akutipangira ma pepala amenewa kuti atipezele ndege yomwe adzabweretse mapepalawa mdziko muno pa 26 March, 2021 koma atiuza kuti zakanika.

“Akuti atafufuza ma kampani onse andege kumeneko, zapezeka kuti pa 26 March palibe ndege yomwe ingabweretsa ma pepalawa kuno ndipo ndege yomwe yapezeka ndi yapa 21 March, choncho tikudziwitsa magulu onse okhudzidwa zakusinthaku, ” watelo Mwafulirwa.

A Mwafulirwa ati posachedwapa MEC ibweraso poyera kudziwitsa dziko komaso magulu onse okhudzidwa pa chisankho chapaderachi zakomwe ma pepala oponyera votiwa akasungidwe akafika mdziko muno.

Dziko lino likupangitsa chisankho chapaderachi pakati komaso ku mpoto kwa boma la Nsanje ndi ku mmawa kwa boma la Chikwawa komwe bwalo lamirandu linalamura kuti kuchitikeso chisankho china kaamba koti panali zolakwika zina pachisankho cha 2019.

Chisankhochi chichitikaso kumpoto kwa boma la Ntchisi, ku Zomba Changalume, kummwera kwa Lilongwe Msinja, kumpoto chakumadzulo kwa boma la Karonga, ward ya Liviridzi ku Balaka komaso Ku ward ya Chitakale ku Mulanje komwe oyimilira maderawa anamwalira