Sitikupezanso ndalama, adandaula mahule ku Zomba

Advertisement

Ochita malonda ogulitsa thupi m’boma la Zomba lachitatu anapita ku khonsolo ya mzindawu kukadandaula kuti iwo sakupezaso ndalama monga kale kamba ka ndondomeko zomwe boma lakhazikitsa zochepetsera kufala kwa mliri wa Covid-19

Polankhula ndi Malawi24 kudzera pa lamya, mtsikana yemwe iye anati ndi Linda anati zomwe achita a boma kuti malo azisangalalo azitsekedwa 8 koloko madzulo zadzetsa mavuto a nkhaninkhani kwa iwo poti pano sakutha kupeza ndalama monga kale ponena kuti makasitomala awo ambiri amafika m’malowa usiku.

Iye anapitiliza kuti anthuwa pa tsiku amatha kupeza ndalama pafupifupi 20 sawuzande ndipo zikayenda bwino zimatha kupitilira pamenepa, ndipo wati boma liwonjezere nthawi kuti malowa azitseka pakati pa usiku.

Anthuwa, eni malo omwera mowa komanso eni malo ogona alendo anali nawo pa ulendowu ndipo anakatenga kalata yowaloledza kukapeleka madando awo ku khosoloyi komwe anakawuzidwa kuti akalembe bwino bwino madando awo.

Boma la Malawi liri pa kalikiliki kuthana ndi mliri wa Covid-19 omwe ukufala kwambiri ndipo ngati njira yochepetsera kufala boma likulimbikisa anthu kuti asamakhale m’magulu komanso azivala zotchingira ku nkhope ngati akupita m’malo moti muli anthu.

Advertisement