Opezeka ndi Corona 8 athawa pamalo owasungira

Advertisement

Anthu asanu ndi atatu (8) omwe anapezeka ndikachilombo ka corona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19, athawa pamalo omwe amawasungira kwa Kameza mu nzinda wa Blantyre.

Watsimikiza zankhaniyi ndi nkulu wa zaumoyo mu mzindawu Dr Gift Kawalazira omwe ati anthuwa athawa usiku wa lolemba.

Malingana ndi a Kawalazira anthuwa ndi ena mwa anthu omwe angofika kumene m’dziko muno lamulungu lapitali kudzera kuchipata cha Mwanza pomwe amachokera m’dziko la South Africa.

Iwo anati anthuwa atafika pa chipatachi anatengedwa onse kupita nawo kubwalo la zamasewero la Kamuzu komwe anasiyanitsidwa ndi anzawo ena omwe sanapezeke ndi nthendayi ndipo anatumizidwa kwa Kameza komwe kukumasungidwa anthu odwala nthendayi.

Izi sizinasangalatse anthuwa ndipo pakati pausiku anaitanitsa galimoto ya mtundu wa minibus yomwe inakawatenga kumalo komwe anakasiyidwako ndipo ati pakadali pano sakudziwika komwe ali.

“Anthu 8 athawa usiku wa lolemba lomwelo pomwe anaitanitsa galimoto yomwe anakwera mkumapita. Ndiye pakadali pano tigwira ntchito limodzi ndi anzathu a immigration kuti atithandize kupeza komwe kuli anthu amenewa.

“Panopa tawonjezerano chitetezo kwa Kamezako kuti pasakhaleso zovuta zilizonse. Chifukwa choti anthuwa akuyenda mobisala, atha kukhala kuti sakutsata malangizo azaumoyo choncho akupeleka chiopsezo choti atha kufalitsa nthendayi kwa anthu ambiri.” Atelo a Kawalazira.

Iwo anati anthu akuyenera kudziwa kuti ichi sichibalo koma kufuna kuteteza a Malawi ndipo apempha kuti anthu akuyenera kugwirana manja ndi boma polimbana ndikufala kwa kachirombo ka Corona.

Iwo anatsindika kuti azachipatala mothandizana ndi apolisi ali kalikiliki kusaka anthuwa ndipo apempha anthu akufuna kwabwino kuti awadziwitse ngati angadziwe komwe kuli anthuwa kuti anthuwa asalitse nthendayi kwa anthu.

Advertisement