Chiwelengero cha opezeka ndi Corona chafika pa 101


Ku Malawi, chiwelengero cha anthu omwe apezeka ndi kachilombo ka Corona komwe kakumayambitsa matenda a Covid-19 chafika pa anthu 101 tsopano.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi nduna ya zaumoyo m’dziko muno a Jappie Mhango omwe amayankhula lolemba ndipo anati pakadali pano anthu ena 18 apezekaso ndikachilombo ka Corona m’dziko muno.

A Mhango anati mwa anthu 18 omwe apezekaso ndikachilombaka, 15 ndi omwe angofika kumene lamulungu lapitali kudzera pa chipata cha Mwanza pomwe amachokera mmaiko a South Africa komaso Zimbabwe.

Iwo anati wina ndi mzibambo wazaka 26 yemwe wangofika kumene kuchokera ku Tanzania pomwe awiri enawo ndi azibamboso omwe nawoso afika m’dziko muno mkatikati mwa mwezi uno kuchokera m’dziko la South Africa.

Ndunayi inati pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi nthendayi chidakali pa anayi pomwe chiwelengero chaomwe achira ku nthendayi chafika pa 37 zomwe zikutanthauza kuti anthu 60 ndiomwe akudwalabe.

Ndunayi yatiso pofika lolemba pa 25 May, anthu okwana 3,324 ndi omwe ayezedwa kumalo 13 omwe ali m’dzikolino oyezerako kachilomboka zomwe zikutanthauza kuti, mwa anthu omwe awayezawa, anthu okwana 3,223 sanawapeze ndi kachilomboka.

Pakadali pano zadziwika kuti mwa anthu 101 omwe apezeka ndi kachilombo ka corona mdziko muno, anthu oposa 60 adachita kubwera m’dzikolino ali kale ndi kachilomboka pomwe anthu enawo akatenga kachilomboka ali m’dziko mommuno.

A Mhango atsindika ndikunena kuti madotolo akupitilirabe kuyeza anthu osiyanasiya kuti awone ngati ali ndikachilomboka ndipo alangiza anthu m’dziko muno kuti apitilize kutsatira malangizo omwe unduna wa zaumoyo ukumapeleka pofuna kupewa kutenga kachilomboka.