Amalawi akanitsitsa m’bindikilo okakamiza

Advertisement

Anthu m’dziko muno amenyetsa nkhwangwa pamwala kuti iwo sakugwirizana ndi ganizo la boma kuti akhale pa m’bindikilo okakamiza kwa masiku 21 kaamba ka nthenda ya COVID-19.

Izi zikutsatira kulengezedwa kwa m’bindikilowu lachiwiri madzulo pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anati maganizowa abwera pofuna kuchepetsa kufala kwa ka chilombo ka kolona komwe kakumayambitsa matenda a COVID-19.

Mwazina, a Mutharika analamula kuti pa masiku 21 akunenedwawa, anthu asamayendeyende ndipo anati misika ikuluikulu yose itsekedwa koma anati misika yakumidzi idzitsekulidwa koma idzitha ikamati 2 koloko masana.

Koma anthu mdziko muno ayilandira nkhaniyi mosakondwa pomwe ambiri anenetsa kuti izi sizitheka ndipo ati nkwabwino kuti boma libweze ganizo lakeli polingalira kuti anthu amadalira maganyu komaso malonda kuti apeze zakudya zawo za tsiku ndi tsiku.

Ena mwa anthu omwe ayankhula ndi Malawi24 ati atsogoleri sakuyenera kutengera zomwe maiko ena akuchita ponena kuti dziko lino ndilosauka ndipo m’bindikilowu sungatheke ndipo ati nkwabwino boma lipeze njira zina zothanirana ndi kufala kwanthendayi.

A Sibongile Chatha omwe amagulitsa thobwa mtawuni ya Blantyre anati ndiokhumudwa kuti boma silikuganizira za kapezedwe ka chakudya chawo chatsiku ndi tsiku.

“Ndizoonadi kuli korona komano boma linakatiganizira kuti akati tipite ku m’bindikilo enafe tidya chiyani popeza ife sitingakwanitse kuguliratu zakudya za masabata atatu. Ndalama yomwe timaipeza ife ndiyachakudya cha taiku limenero basi,” anatero mai Chatha.

Mbali inayi mmodzi mwa anthu ogwira ntchito ku hotela ya Mount Sochi yemwe anati tisamutchule dzina wati pano apatsidwa tchuthi chokakamiza ndipo adulidwa malipilo awo zomwe ati nzokhumudwitsa ndipo ati akudana koopsa ndi m’bindikilowu.

“Zoonadi nthendayi ndiyowopsa komano fuso langa ndilakuti kodi basi zomwe zingathetse nthendayi ndi m’bindikilo okakamizawu? Ndikuona ngati boma linakaganizira munthu wakumudzi komaso ife apantchito ngakhaleso anzathu ochita malonda,” anatero m’modzi mwaogwira ntchito ku hotela ya Mount Soche.

Pofuna kuonetsa kukwiya kwawo paganizo laboma la m’bindikilowu, anthu ochita malonda ku Mzuzu komaso ku Mangochi lachinayi anachita zionetsero ponena kuti iwo salora kupita ku m’bindikilowu.

M’mawa wa lachisanu kunaliso chipwilikiti ku msika wa Limbe komwe ochita malonda anachitaso zionetsero zomwe mwazina anatseka misewu ndikuyatsa mateyala ndipo anenetsa kuti iwo m’bindikilo okakamizawu sukuwakhudza.

Matthews Govati yemwe amagulitsa mbatatesi munsikawu anati: “Ife sitiloratu maganizo awowa chifukwa kuti tizikangokhala kunyumba tikafa ndinjala ndiye ndikwabwino kuti tife ndinthendayi kusiyana ndikufa ndinjala.”

Dzulo anthu ena ku Mangochi ndi ku Mzuzu anachita zionetsero posakondwa ndi ganiza loti pakhale m’bindikilo.

Pakadali pano bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati likatenga chiletso kuti dziko lino lisakhale pa m’bindikilowu ponena kuti kutero kubweretsa mavuto adzaoneni pakati pa anthu.

Koma ngakhale anthu akukanitsitsa m’bindikilowu, Lachinayi akuluakulu a apolisi komaso asilikali ati iwo ndiokozeka kugwira ntchito yawo mogwirizana ndimalamulo payemwe angapezeke akuphwanya zomwe zanenedwa za m’bindikilozi.

Anthu khumi, asanu ndi mmodzi (16) ndiomwe atsimikizika kuti anapezeka ndi nthenda ya COVID-19 mu mdziko muno pomwe awiri anamwalira ndi nthendayi.

Advertisement