Mgwirizano omwe tikufuna ndi oti Chilima akhale patsogolo – phungu wa UTM

Advertisement

M’modzi mwa aphungu anayi omwe chipani cha United Transformation Movement (UTM) chinapeza pa zisankho chaka chatha, wati akufuna kuti mgwirizano omwe chipani chawo chingalowe, mtsogoleri wawo a Saulos Chilima akhale pamwamba osati wachiwiriso.

Izi zikutsatira chigamulo chabwalo la milandu ku Lilongwe sabata yatha pa mlandu wazotsatila zachisankho cha mtsogoleri wadziko omwe unakomera a Chilima komaso mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera.

Pa chigamulochi, khothi linalamura kuti ondandaulidwa oyamba omwe ndi bungwe la MEC apangitseso chisankho china cha mtsogoleri wa dziko pasanathe masiku 150 ponena kuti chisankho cha pa 21 May chaka chatha bungweli linalakwitsa zambiri.

Potsatira chigamulochi, atsogoleri azipani zingapo kuphatikazapo a Chilima abwera poyera ndikunena kuti zipani zawo zili zokozeka kulowa mumgwirizano ndizipani zina zomwe zingafune kupanga chomcho.

Poyankhula pa zoti chipani chawo chitha kulowa mumgwirizano ndizipani zina, phungu wa UTM kumadzulo kwa mzinda wa Blantyre, a Steven Mikaya ati iwo salora kuti a Chilima akhale pambuyo pamunthu wina mu mgwirizano omwe angalowe.

Phunguyu waoneka akunena izi pa kanema wina yemwe anthu pamasamba amchezo akugawana ndipo amayankhula izi sabata yatha pomwe anapangitsa msonkhano mbali imodzi ya dera lake.

A Mikaya ati ngati izi zingachitike choncho zikhala zokhumudwatsa kwaiwo kaamba koti a Chilima anakhala kale wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko chomcho akufunikano kukhala patsogolo osati udindoso omwewo.

“Nde mgwirizano omwe ife tilore kuno kuchigawo chakummwera ndi oti a Saulos Chilima akhale patsogolo ngati mstogolori. Wakhala kale wachiwiri 2wa dziko nde akhaleso wachiwiri wa dziko?

“Wathu akhale patsogolo basi. Pepani ndaswa ndondomeko koma ndimafuna ndinene zimene anthu tikufuna kuno ku chigawo cha ku m’mwera,” watelo Mikaya.

Posachedwapa kanema winaso pamasamba amchezo wawonetsa wachiwiri kwatsogoleri wachipani cha UTM a Michael Usi omweso amayankhula pamsonkhano, akuwuza anthu anthu asadandaule ngati chipani chawo chingalowe mumgwirizano iwo mkuchosedwa pa udindo wawo.

Pakadali pano palibe chipani chomwe Chabwera poyera kunena za mgwirizano uli onse ndi zipani zina.

Advertisement