Likakuona litsilo siikata: Mutharika alepheretsa msonkhano wa Chakwera


Patatha sabata mvula italepheretsa mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha Malawi Congress (MCP) a Lazarus Chakwera kuyankhula kwa owatsatira, a Chakwera akakamizidwa kupangitsa msonkhano wawo lamulungu mmalo mwa la loweruka.

Izi zadza khonsolo ya m’boma la Mangochi itauza chipani cha MCP kuti msonkhano omwe umayenera kukhalapo mawa uchitike tsiku lina.

Chipani cha MCP chinalembera kalata khonsoloyi kupempha kuti mtsogoleri wake a Chakwera azachitise misonkhano mubomali loweruka pa 1 Disembala.

MCP inapempha khonsoloyi kuti motsogozedwa ndi a Chakwera chikufuna chizapangise misonkhano yoimaima m’bomali kenaka ndikukapangitsa chimsonkhano cha mzanga undipondera mwana pa sukulu ya Mbwadzulu.

Mu zomwe chipanichi sichimayembekeza, chakanizidwa kukapanga misonkhanoyi loweruka kamba koti mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika nawoso akukapangisa misonkhano yoimaima loweruka.

Malingana ndichikalata chomwe khonsoloyi yatulutsa, a Mutharika azapangisa misonkhano yoimaima ku Monkey Bay tsiku lomweli.

Khonsoloyi yati ndiye ndizosatheka kuti pomwe a Mutharika azakhale akupangitsa misonkhano yawo, a Chakweraso azakhale akupangitsa yawo mu boma lomweli.

“Takulemberani kuti tikupempheni kuti musinthe mpaka tsiku lina la msonkhano wa mtsogoleri wa chipani cha MCP kamba koti mtsogoleri wa dziko lino nayeso akhala akupangitsa misonkhano mmalo omwe a Chakwera amafunaso kuti apangitse misonkhano yawo” yatelo kalata ya khonsolo ya Mangochi.

Kalatayi atikitira ndi bwana mkubwa wa bomali a Dominic Mwandira.

Sabata latha tsiku longa lomweli a Chakwera analephera kuyankhula ku chinantindi cha anthu omwe anasonkhana pa Mjamba ku Blantyre kamba ka mvula yomwe inasokoneza msonkhano wawo.