“Kaliati waputa mwana mulhomwe” – Ngolongoliwa

Advertisement
Patricia Kaliati

Mfumu yaikulu ya a Lhomwe mudziko muno Paramount Chief Ngolongoliwa yaopseza m’modzi mwa mamembala a United Transformation Movement (UTM) a Patricia Kaliati ponena kuti akhale osamala chifukwa aputa mwana mu Lhomwe.

Chinatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga mchakuti a Kaliati anathokoza kumtundu wa anthu omwe anasonkhana pa bwalo la Masintha Ku Lilongwe pa zomwe anawachitira a Ngolongoliwa komaso munthu wa malonda a Leston Mulli.

Senior Chief Ngolongoliwa
Senior Chief Ngolongoliwa: Kaliati waputa mwana mu Lhomwe.

A Kaliati anauza chikhamu cha anthu chomwe chinasonkhana pa bwaloli pa 21 Julaye pokhazikitsa gulu la ndale la United Transformation Movement (UTM) kuti mfumu ya a lhomweyi ndiyomwe inawauza kuti akhale kumbuyo kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima.

Izi zinakhumudwitsa mkulu wa gulu la a Lhomwe mdziko muno a Muchanya Mpuluka omwe anaopseza kuti ngati a Kaliati sapepesa pa zomwe anayankhulazo, gulu lawo la a lhomwe likachita m’bindikilo Ku nyumba yawo koma a Kaliati anatemetsa nkhwangwa pamwala kunena kuti iwo sangapepese.

Poyankhula pa nkhaniyi loweluka lapitali pa wailesi ya kanema ya dziko lino, a Ngolongoliwa anati iwo ndiokhumudwa kaamba kazomwe anayankhula mneneri wa UTM you ndipo aopseza kuti achita chinthu chomwe sanachitchule.

Iwo anati zonse zomwe ananena a Kaliati pa msonkhano wawowo zokhudza iwowo pa nkhani ya a Chilima ndi bodza la mnkunkhuniza.

“Ine ambwiye sindikudziwa kalikose pazomwe akunena a Kaliati ndipo ndikufuna ndimuuze kuti ameneyu aonaso chifukwa waputa mwana mulomwe. Ngati iyeyo simulomwe koma apapa adziwa kuti ine ndi mulomwe weniweni wapaphata.

“Zonse zomwe akumanena sikuti sindikuzimva, ndikumazimva ndithu koma ndikufuna ndikuuzeni ambwiye kuti zonsezo ndizabodza ndipo palibe chomwe ndidziwa ine ndipo ameneyu asasewere ndiine,” anatero Ngolongolowa.

Atafusidwa ndi mtolankhani yemwe amacheza naye pa kanemapo za chinthu chomwe achitecho ngati amatanthauza zokhudza matsenga, mfumuyi inakana ponena kuti sanena chinthu chomwe achitecho koma anatsindika kuti apanga chinthu china chake pa a Kaliati.

A Ngolongoliwa ananenaso kuti ndiogwilizana ndimaganizo omwe apangidwa okapanga m’bindikilo ku nyumba kwa a Kaliati ngati sangapepese pa masiku asanu ndi awiri omwe anapatsidwa omwe atha dzulo lamulungu.

Iwo anati iwo akuikila maganizowa kumbuyo kaamba koti palibe mwana aliyese yemwe amangokhala ndikumayang’anira bambo ake akunyozedwa ndimunthu wina.

Mfumu ya a Lhomweyi inatsutsaso kwa mtu wa galu zomwe akhala akuyankhula a Kaliati zoti iwowo pamodzi ndi a Mulli akhala akukumana nawo ndikumakambilana zokhala kumbuyo kwa Chilima.

Padakali pano a Kaliati sanayankhepo pa za chiopsezo chomwe yanena mfumu yaikulu ya alomweyi.