Zilipo 2019: A Usi alowa ndale, a Chilumpha ayambitsa chipani

Advertisement
Michael Usi

Kuli kanthu konthula nchala chaka chamawa pomwe zikusonyeza kuti dziko lino labadwitsaso chipani china pomwe a Michael Usi alowa ndale.

Lamulungu lapitali pa 7 Januwale, m’modzi mwa anthu odziwika bwino pa zisudzo, a Usi analengeza kuti akusiya zisudzo ndipo akuyamba ndale komaso akuyambitsa chipani chawo.

Michael Usi
a Michael Usi alowa ndale.

A Usi omwe amadziwika bwino ndidzina loti Manganya ati apangitsa kale zovala zomwe azigawe dziko lose la Malawi zowauza anthu kuti nthawi yosintha zinthu ndi ino.

A Usi omwe ndi mkulu wa bungwe LA Adventist Development and Relief Agency (ADRA) akana kubwera poyera ngati ali ndimaganizo odzapikisana nawo pampando wa mtsogoleri wadziko pa zisankhozi.

“Ndawadziwitsa kale akuluakulu onse a ADRA zakutula pansi kwa udindo wanga, koma andiuza kuti ndidikile kaye pang’ono ndiye naneso ndawauza kuti ndagwira ntchito kwambiri ndiiwo ndipo ndinthawi yoti apezeso Munthu wina,” atelo a Usi.

Patangodutsa maola ochepa chilengezeleni izi, namandwa winaso pankhani zandale a Cassim Chilumpha nawoso alengeza kuti ayambitsa chipani chawo.

A Chilumpha ati chipani chawo chatsopanochi chiziziwika ndi dzina loti Assembly for Democracy and Development.

Mkuluyu yemwe anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko wabweleratu poyera kuti chipanichi chizapikisana nawo pa zisankho zomwe zikubwerazi.

Iwo anakhudzidwapo ndikubedwa kwandalama zokwanira K187 miliyoni zaboma zomwe boma linkafuna kumangira sukulu koma bwalo lamilandu silinamupeze olakwa pa mulanduwu.

Pakadali pano dziko lino lili ndizipani zopitilira makumi anayi (40) chiwerengero chomwe ndichokwera kwambiri.

Advertisement

62 Comments

 1. Kukhala Ngat Zamasewero Wasiya, Zovla Nsalu Pa Sikirin Wasiya Km Ukanatisimikizir Kt Tisamawerengere Za Masewero Anu Chemanganya.

 2. Pempho langa nali Mr Usi ngati mungandivere.Ngati mungathe yambiysani chanu chipani mujowine tizipani tilipanoti nditephera. Tikungoba anthu ndi kumavutika kapena ngati mungakwanitse joinani MCP basi chifukwa ndi chipani chokhacho chomwe chikuoneka ngati bolaniko koma zinazi zidzakugwetsani.Zikomo

 3. Ndiye Ausi adzaima ngati president kapena mp? Takulandirani Ausi mmunda umeneu nanu mukolole chanu chithumba mudzikadya ndi banja lanu komamso ndi ntundu wamu ena akukulukutika ndi umphawidziko lomwelino.Pemene anthu adzidzafa mzipatala za mdziko lino chifukwa chosowa mankhwala inu mudzidzakhala muli mu ndege ulendo wokanjoya ku America.Takulandirani nanuso chithumba cha cashgate akhale pillow wanu.

 4. What is the name of Manganya’s Party please? Need to join this party ndidzakhale Minister mmoyo winawo.

 5. Let’s not judge Mr usi because we are living in democratic world and he has the right to do so since he is the citizen of malawi and also let’s not confuse his commedy talents with serious business,They are different he might be good enough to bring some change

 6. Kma 2019 ziliko ma coach akusiya akufuna u mp maplayer akusiya akufuna akhaleso mp wina ndi uyu wama drama nayeso kma kusala munthu.2919 kuvuta

 7. Chipani chamasewero ngati pansalu palembedwa wakudya chake alive mulandu nde kuti pali zanzeru pamenepa?? Kungoonetseratu kuti zachibwana zenizeni

 8. If I can see very well beyond…joining politics of Mr manganya……………….what I find out it’s regreting

 9. Zaozimenezo ine sindidzapita kovota chifukwa ndavotakunakwanabasi Tikungoikambava m’mipando ndatopa nazo zimenezo patsikulo ndizakhalandilikumunda kokasosa.

 10. Yambitsanidi, otibera amphawi ife achuluke ife kwanthu kukhala kumangolira basi. Phindu muziliwona nokha basi kumipando kwanuko, anthu okhala ndi chisoni ndi amphawi mukakhala kunja kwa boma. Koma mukangolowa m’bomamo, chisoni chonse chimatha ndiye tiyenazoni ndale zapaMalawi ndiye zimenezo

 11. ofunika malamulo asinthe coz zipani zachuluka abale angofuna nda;lama ofunika zinazi kuzathesa zitatu fyn enawa ndi dyela lakula

 12. Ndalama yavta amwene,anthu akwona kt politics nd deal,koma alipo ena omwe akfna kutukula dzkoli,Yehova athandize amenewo,nt adyerawo,.

 13. kkkkkkk Ndili Jz komano panopa ndikuchosera myezi ndi kubwera popano tibwezemo nafe tiwadyere andalewa! cz iwowa amatidyera kwa 5 yrs.ife tiwadyere kwa myezi yochepa #Utsi uthenga ndi umenewo ndikubwera tipanga guru la macadeti lomwe tizikupusisa naro, kukoma kwake uzayimiraso dera lakwanthu ku #Mj uko! ndiye uziwaso sitikunyengerera kkkkkkkkk Achinyamata azanga inuso omwe muli madera ena pangani chimozimozi kunja kwacha uku! tiwadyere amaza okha kumamizi timakhalaku! paja samawoneka akawina awa! ndiye kubwezamo zazaka 5.

 14. sopusa!!!! mumpeze okuvotera anthu oipa inu..mungoyambitsa zipani muli phee ndi cholinga chodyera masuku pa mutu anthu osauka osati kuthandiza dziko..anthu akubha inu…judgement is waitng on you kumwamba….bola muzidzalapa mukamadzamwalira kkkkk…

 15. Ineso ndayambitsa changa zanga phee united vote ndimumtima ofunika bussnes kwa andale nose bwerani pamsika wamavote kuyambira k2.6 million osanenelera

 16. Mwatsala ndi inu kuti mulengeze chifukwa zimachita kuwonetseratu kuti ndalezi munalowa kale.tsiku lilironse nkhan izingokhala imodzimozi mulibe nkhan dzina zoti mungalembe

 17. A Utsi Inu Pitilizan Kulandila Ma Fundingwo Mukukhumbazo Simungakwanitse Coz Si Sewelo Lomangobwebwetuka Opanda Okutsusa Kapena Kukudzuzula

 18. ussi amaoneka ozindikilako, atha kulongosolako zinthu, ofunika kumuyesa Kaye pa kaudindo kakang’ono kaya u councillor kaya u MP

 19. A Utsi Inu Pitilizan Kulandila Ma Fundingwo Mukukhumbazo Simungakwanitse Coz Si Sewelo Lomangobwebwetuka Opanda Okutsusa Kapena Kukudzuzula

 20. Koma iyi nkani yoti aliyense azingoyambitsa zipani mmene afunira ni no bwino iyayi .Zipani mbwee kumangozunguza nazo anthu mitu basi. What change will the new party/ies bring on the table ? It’s sickening ! Scrap all these useless parties . Reduce the number of parties to three major ones . Keep things simple

Comments are closed.