Mfumu ya zinyau ipereka mphatso kwa oyikonda


Tay Grin: Wapereka phukusi la nyimbo zisanu ndi imodzi kwa a Malawi .

Mu nyengo yino yachisangalalo yimene kumakhala zikondwelero za masiku a Khirisimisi ndi Nyuwele, mfumu ya zi Nyau sinalore kuasiyasiya oyikonda powapasa mphatso.

Mfumuyi imene dzina lake lili Limbani Kalilani, yapereka phukusi la nyimbo zisanu ndi imodzi kwa a Malawi amene amakondwera ndi mayimbidwe ake. Iyo yachita izi kuti anthu asangalale mwamkokomo mu nyengo yino.

Kalilani amene amatchuka ndi dzina loti Tay Grin, waimba mothandizana ndi akatswiri angapo amayiko akunja.

Ena mwa oyimbawa ndi Bebe Cool wa Ku Uganda, Orezi wa Ku Nigeria ndi Jay Rox ochokera mu dziko la Zambia.

Katswiriyu wayimbaso mothandizana ndi a Malawi amzake monga Sonyezo Kandoje amene amadziwika kuti Sonye, komaso Gemini Major amene amakhala mu dziko la South Africa.

Mphatso yi yaperekedwa lolemba usiku kudzera pa pologalamu ya pawailesi yotchedwa made on Monday. Ndipo analandira mphatso yi mmalo mwa a Malawi ndi bambo Joy Nathu amene ali muulusi wapologalamuyi.

Nyimbo zomwe zikupezeka mu phukusili nazi; 21, Tawe, Ssinaziona, One more touch, Hallelujah ndi Balenciaga. Ndipo anthu apereka maganizo osiyanasiyana pa nyimbozi.

Imodzi mwa Nyimbodzi, one more touch ndi yomwe ili yodziwika kwambiri kamba koti inatuluka mwachangu. Kanema wa nyimbo yi anafala paliponse mdziko muno.

 

26 thoughts on “Mfumu ya zinyau ipereka mphatso kwa oyikonda

  1. Kukweza kamba mu mtengo man awa satha kuyimba ine ndiye ayi kwawo komweko bola ndizivera TSAR LEO fana waluso uyo wosati chitelera chomwe amayimba ada kaya amati ndi hip hop kaya ndi beni

  2. naneso ndimaikonda hvy mfumui.koma fuso mkumati iyoy imadziwa zimenezo,nanga oikonda ake ndiati omwe alandire mphatsoo? mwina ndine amene!

    1. Fredo ali ngati bambo ake Kamlepo…. always making noise but has no legacy….
      Nkona akumapanga tima show taulere kuli kugula fame…. mtchana wamakape

Comments are closed.