Chimanga chonse chija chinayi wajomphapo Tambala wakuda, ndipo ngati a chipani cholamula amayesa kuti a Malawi adakali mtulo tsopano adziwa dziko lidasintha.
Chipani cholamula cha DPP chaonetsedwa mbwadza, kapena kuti mbonaona, pa chisankho chapadela chomwe chinachitika mu madera osankhika lachiwiri.
Kongeresi ndiyo yaonetsa mdima DPP powambwititsa ku madera asanu pa chisankho chomwe chinachitika ku madera asanu ndi limodzi. A DPP angotola dera limodzi lokha ku Dedza uku la khansala.
Ku dera la Nsanje Lalanje ndiko kunali kanthu kokanthula n’chala kamba a DPP amafuna kupimana mphamvu ndi a Kongeresi amene atola khang’a Sidik Mia.
Uku ndiye a DPP nawo awona mbwadza, mnyamata wa Kongeresi Lawrence Sitolo atangokwangulamu zonse ndi kuwasiyila zidutswa a DPP amene anaimika Mayi Ganda ngati owanyamulila mbendera.
A katswiri a ndale anena kuti kugonja kwa DPP, maka ku Nsanje ndi ku Ndirande kwaonetsa kuti a Malawi sali okondwa ndi ndale za chipanichi.
psa psa psa koka koka koka zan’gana ku dazibhomo n’gombe eh nde kuti ikhale mmalo suuvitya kwake
eetu wamkulu akakhala kuipa osakokera kabudula muntunga imamuuza m mphepo. mavalo akazizibwa. koma nde hati attaki.vimangeni vimbano ivi vasakaza dziko. vifwnthe vanu