Boma ndi lokhonzeka kunyetsa onse ofukula mchenga

Advertisement
Sangwani Phiri

A ku unduna woona za chilengedwe, mphamvu ndi migodi ati iwo satopa kulimbana ndi anthu onse amene ali pa kalikiliki kufukula mchenga.

Malinga ndi a Sangwani Phiri amene amayankhulila undunawu, iwo ati undunawu ndi okhumudwa ndi khalidwe lovuula mchenga maka m’mbali mwa mtsinje.

Sangwani Phiri
Sangwani Phiri wati udunawu ndiokhumudwa ndi khalidweli.

Iwo ati boma ndi lokhudzika ndi mchitidwe umenewu kamba koti umaononga chilengedwe.

A Phiri ati ngati boma, sanyengelela anthu onse opezeka akuchita makhalidwe amenewa.

Iwo apemphanso mafumu ndi a Malawi onse kuti akhale okonda dziko lawo ndipo agwilizane ndi boma pothetsa mchitidwewu.

Advertisement