Sindinapinyolitse chipani ine – watelo Atupele

Advertisement
Atupele Muluzi

Mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF), a Atupele Muluzi ati iwo sanapinyolitse chipanichi kwa a Mutharika.

Atupele Muluzi
Atupele: Sindinapinyolitse chipani

A Muluzi amene ndi nduna mu boma la a Mutharika anauza anthu ku Ndirande kuti iwo ndi anyamata a ndale zamakono zofuna kumanga dziko.

“Zikatha zisankho, timayenera kuyamba kumanga dziko. Ine ndikugwila ntchito ndi a Mutharika kuti tithandizane kumanga dziko,” anatelo a Muluzi.

A Muluzi anati ndi ndale zachikale zomakokanakokana chifukwa choti munalikhilana mumchenga pa chisankho.

“Dziko likutsogola ndiye machitidwe athu a ndale nawo atsogole, tizigwilila ntchito limodzi,” anatelo iwo.

Pa msonkhano omwewo, a Muluzi analandila a Clement Chiwaya amene anali nduna nthawi ya a tcheya koma anapita kwa amayi.