Ndine okonzeka kunjatwa – atelo Mayi JB

Advertisement
Joyce Banda & Oswald Lutepo

Mtsogoleri opuma wa dziko lino Mayi Joyce Banda amene dzulo Apolisi aulula kuti aupeza unyolo wa msinkhu wawo ati iwo sakunjenjemela ndipo ndi okonzeka kuuvala unyolowo.

Joyce Banda
Mayi Joyce Banda: Ndine okonzeka

Malinga ndi Bambo Andekuche Chanthunya amene amalankhulila mayi Banda, a Banda ati sachita mavuvu ndipo azipeleka kwa Apolisi akangopatsidwa chikalata chomwe bwalo linapeleka kuti awanjatile.

“Padakali pano, chikalata chomwe akuti adatenga ndipo chinawapatsa mphamvu Apolisi kuti akwizinge a Banda sanachilandile. Iwo angomva kwa anthu, koma akachilandila, akazipeleka okha ku Polisi,” anatelo a Chanthunya.

A Chanthunya anaonjezelapo kuti a Banda ndi munthu omvela malamulo ndipo kukhala kwawo kwa kunja si kuthawa milandu.

Apolisi anaulula ku mtundu wa a Malawi pa 31 Julaye kuti iwo ali ndi chikalata chowapatsa mphamvu zonjata mayi Banda pa nkhani yokhudzana ndi kusolola, ya kashigeti.

Apolisi anati anthu angapo anaulula kuti a Banda anachitapo gawo pa kusolola chuma cha boma.

Malipoti akuti a Banda padakali pano ali mu dziko la Amereka.