Zotsatira zakafukufuku wa a polisi m’dziko muno zaonetsa kuti anthu 331 ndi omwe amwalira pa ngozi za pa msewu zomwe zachitika mu miyezi isanu chaka chino.
Izi ndimalinga ndi otsatira kwa mkulu ofalitsa nkhani za a polisi m’dziko muno a Thomeck Nyaude.
A Nyaude ati a polisi ndi omwe anachita kafukufukuyu kuyambira mu mwezi wa Januwale kufikira mu Meyi.
Izi akuti ndi ngozi zochuluka poyerekeza ndi ngozi zomwe zinachitika mu miyezi ngati yomweyi chaka chatha.
A Nyaude anaonjezera kuti gwero la ngozi zoterezi ndi kuyendetsa galimoto munthu ataledzera komanso kunyozera malamulo a pa msewu.
Ngakhale chiwerengerochi ndichokwera kale, pali nkhawa yoti nambalayi ikwera kwambiri potengera kuti apolisiwa sanawerengere ngozi zimene zachitika mwezi wa Juni.
Mwezi watha ndi mwezi umene anthu ambiri m’dziko muno adzaukumbukire chifukwa chakuchuluka kwangozi za pansewu.
M’mweziwu, sipamadutsa masiku osamva zakufa komaso kuvulala kwa anthu pangozi zapansewu zomwe zinapangitsa akuluakulu owona za pansewu kukhwimitsa malamulo a pansewu zomwe sizinaphule kanthu kwenikweni.
Anthu opitilira makumi atatu ndiomwe atisiya pangozi zapansewu mu mwezi wa Juni okha, chiwerengero chomwe ndichokwera kwambiri.
Zoopsa ndithu
May soul rest in peace
Ask boma about it
We need a public holiday , for everyone to seek God’s mercy on our Malawi
Yeah
Too bad
Amwalira kapen anamwali sindikumvesesa pamenepa chichewa chimandivuta ndithandizen guyz
Its too much esh 5 months ! Very bad
Ndizovesa chison chaka sichinate manso palibe nambala yaziwembu zasatanc zawojeza.
zomvesa chisoni ambuye atithandize
shameful
+ 8 alelowa, ai taluza anthu mchakachi, nde sichinathe nanga ena akufa daily nzipatalawa, Ai satana waingwiradi ntchito,.
Zolilisa kwambiri
Azibusa ndi mashekhe tisiye zonyozana zipembezo kona tigwilane manja Mw yu timuikize mmapemphelo
kodi kumakhala kuyitanira malonda mukamati more at
so bad news ku malawi
rip
mungoti read more at.read more at….kodi muzitiuza nafr apapa kodi beanji.mesa ndi news griuo iyiyi?.
Kkkkkkkkkkkk a wuzen man
Inu Ndi Dhilu.
Amationjeza kwambili
kkkkkk
+ 8 lero ku BNS satanic iri pa mapwando.