Pavuta pa msika: Shuga wasowa

Advertisement

Zativutanso!

A Malawi ali pakalikiliki kuthamangila ku ma okala kuti apeze  nawo mwayi ogula shuga yemwe akusowa zedi mdziko muno.

Shuga wasala ochepa zedi mu magolosale aakulu ngati Shoprite, Peoples, Sana Cash and Carry komanso Chipiku.

sugar
Akusowa pa msika.

Malingana ndi  maripoti, izi zili chomwechi  chotele kamba koti kuli mpungwepungwe pa nkhani za mgwilizano wa pakati pa kompani yomwe imapanga shugayu ya Illovo komanso makampani onyamula shuga kuchokera kumafikitale kupitisa mmisika.  Koma a Illovo sanayankhulebe kalikonse pa za nkhaniyi.

Mu Shoprite mwachitsanzo munthu sakuloredwa kugula mapaketi opitilira asanu ndi limodzi (5) . Izi zaikidwa kuti aliyense aguleko shugayu yemwe akugulidwa ndi anthu mokanganiliana.

Izinso zapangisa kuti shuga afike pa mitengo ya K950 komanso K1000 kupyole mtengo ovomelezeka wa K750.

Mmene zililimu, pofika sabata la mmawa, shuga akhala atatheratu kamba koti mumagolosale ambiri watheratu.

Pakali pano bungwe lowona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) lati kampani ya Illovo iyenera kunena ku mtundu wa a Malawi vuto leni leni la kusowa kwa shugayu.

IIllovo ndi kompani yokhayo yomwe imapanga shuga ku Malawi.