Ochemerera wa Bullets, Billy One apepesa ku mtundu wa Malawi


Billy One

Modzi mwa ochemelera a timu ya Nyasa Big Bullets, Beleti Severe yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Billy One wapepesa ku mtundu wa a Malawi pomenya mlembi wamkulu mu unduna wa zantchito, zamasewero komaso zomangamanga a Sam Madula.

Billy One anamangidwa lolemba atakuntha  mbama mlembi wa mkulu mu unduna wa zantchito, zamasewero ndi zomangamanga, patangosala phindi zochepa kuti Nyasa Big Bullets ithambitsane ndi Be forward Wanderers mumasewera omwe amalimbirana bus pa Bingu National stadium mu mzinda wa Lilongwe.

Billy One
Billy One (Mu buluku lakuda) ku khoti ku Lilongwe.

Mawu ake Billy One wati iye ndi okhudzika komaso wapempha  mtundu wa a Malawi komaso a Madula kuti amkhululukire pa zomwe anachita lolemba lapitali.

“Ndikupepesa kwa a Malawi onse omwe anamva zomwe zinachitikazi, komaso ndikupepesa kwa a Madula omwe ndinawalakwira komaso banja lawo lonse ndikupempha kuti andikhululukire pa zomwe ndinachita,”Billy one adauza wailesi ina yodziwika bwino.

mmawu ake Billy akuti sakudziwa chomwe chimamuchitikira kuti  afike pomenya  mlembi wa mkulu mu unduna wa zantchito, zamasewero ndi zomangamangayu  kamba koti mutu wake unali utasokonekera ndi utsi okhesa misozi omwe unaponyedwa pa gate pomwe anthu ena amasokoneza.

“Sindikuziwa kuti zinakhala bwanji kuti ndimenye munthu wa mkulu ku unduna wa zamasewero chifukwa pa nthawi yomwe zimachitika izi mutu wanga unali utasokonekera ndi utsi okhesa misozi (tear gas) yemwe anaponyedwa pa gate pomwe anthu ena amasokoneza.

“Ndipo sindimaziwa chilichonse chomwe ndimachita komanso ndinali odabwa nditazindikira kuti ndinamenya mlembi wa mkulu mu unduna wa zamasewero chifukwa pa nthawi yomwe zimachitika izi sindimayakhulana ndi mlembiyu ndikupepesa kamba ka zomwe ndinachita,” adaonjezera Billy One.

Billy one yemwe ali pa bail pakadali pano azakaonekeraso ku bwalo la milandu pa 21 January 2017 pomwe akakhale akupitiliza kuyakha mlandu ovulaza munthu.

140 thoughts on “Ochemerera wa Bullets, Billy One apepesa ku mtundu wa Malawi

  1. Indeed kupepesa uku nkwaboza wabullets sazatheka they dont av manners they are 100% ignorant thats y they called themselves palestines they aren^t malawians mmalawi amakhala wa ntendere dont trust bullets fans

  2. Billy one knows why he had to hit him. That’s not the correct reason. He’s just saying that coz the so called victim has some powers next time don’t slap him use a gun if possible

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading