22 October 2016 Last updated at: 1:08 PM

A Mutharika alalatira Zodiak, awuza a Malawi kuti iwo ali bwino

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika dzulo analankhula ndi atolankhani a dziko lino masiku asanu chifikileni mdziko muno.

Mtsogoleriyu anafika mu nyumba yomwe munali atolankhani akuoneka wanyonga kusiyana ndi mmene amaonekela lamulungu atafika ku Malawi kuno.

Iye atafika kutsogolo anaimika manja ake awiri mmwamba ati chitsimikizo choti anali moyo komanso wangwiro. Pamene anafika lamulungu ku Malawi kuno, a Mutharika amakanika kugwilitsa ntchito dzanja lawo lamanja zimene zinapangitsa ambiri kuganiza kuti mkuluyu anadwalikadi.

Peter Mutharika

A Mutharika; Alankhula za u moyo wao.

“Ine ndili bwino, ndinaonedwa ndi madokotala amene andiuza kuti ine ndili bwino ngati ka mnyamata ka zaka makumi atatu (30),” anatero a Mutharika.

“Ngati ndinali ndi vuto, inali nyamakazi basi. Ndinapita ku chipatala kumene anaganiza zongondibaya ka jekiseni basi, ndi kamene kamapeleka phuma lamulungu lija ku dzanja langa la manja,” anatero uku azimayi akuimba nthungululu.

“Monga mukudziwa, nyamakazi siipha munthu, kapena mwina ku Zodiak,” anaonjezela.

A Mutharika ananena kuti atolankhani a ku Zodiak anachulutsa mabodza ma za umoyo wawo, ena kutchukitsa kuti atsamaya kumene.

Iwo analangiza wailesi ya Zodiak kuti isinthe mawu ozitamilira kuchoka ku ‘Zikachitika mumvera kwa ife’ ndi kukhala ‘mabodza mumvera kwa ife’.

A Mutharika anaonetsa mkwiyo wawo ndi anthu a Zodiak pamene anamudula mtolankhani wa Zodiak asanamalize kufunsa mafunso. Mtolankhaniyu, a Tereza Ndanga ananena kuti ali ndi mafunso atatu, koma atangofunsa funso limodzi, a Mutharika ananena kuti mtolankhani wina afunseko funso.

Anthu otsutsa a Mutharika ena apitirizabe kunena kuti a Mutharika akudwala ndipo dzulo anamwa chabe mankhwala a mphamvu kuti aiwaleko matenda awo.

Koma anthu ambiri amene anaona a Mutharika dzulo atsutsa zimenezi ndipo ambiri atsimikiza kuti mkuluyu ali bwino.

Kupatulapo nkhani ya umoyo wawo, a Mutharika anayankhukaponso za kuzimazima kwa magetsi ponena kuti boma lawo likubwela ndi njira zatsopano zoonela kuti vuto limeneli lithe.  194 Comments On "A Mutharika alalatira Zodiak, awuza a Malawi kuti iwo ali bwino"