Musapepese a Malawi, kapepeseni DPP mubwelele – Kalindo wauza UTM

Advertisement
Bon Kalindo

Wochita ndale Bon Kalindo wati zomwe chachita chipani cha UTM popepesa kamba ka malonjezo osakwanilitsidwa, ndikuwatengera aMalawi kuntoso, ndipo wati chipanichi chikapepese komaso chibwelera ku DPP komwe chinachokera.

A Kalindo amayankha pa zomwe mlembi wamkulu wa United Transformation Movement a Patricia Kaliati anayankhula pa msonkhano omwe chipanichi chinachititsa m’boma la Zomba kumathelo a sabata yatha.

Ku msonkhanowu, a Kaliati anati; “Tinkanena kuti anthu adzadya katatu ndi Ife, omwe ananena za ma mega farm ndi Ife, Tikuvomela kuti ndi Ife, omwe tinkati feteleza mudzagula wotchipa. Tikuti pepani, wapakaliyala samaimba belo.”

Koma Kalindo kudzera mu kilipi (audio clip) yomwe watulutsa Lachiwiri pa 21 May 2024, wati kupepesaku ndikosaveka kamba koti chipanichi chachita izi mochedwa zinthu zitayipa kale.

Mkuluyu yemweso amadziwika bwino ndi dzina lake la pa zisudzo la Winiko, wakumbutsa chipanichi kuti madzi samayiwala khwawa ponena kuti UTM ikuyenera ibwelere ku chipani cha Democratic Progressive komwe inachokera.

“Ngati pali bwezi la MCP ndi UTM. Nonsenu ndinu amodzi. A UTM musapange zowapusitsa aMalawi, pano anthu anasukusula muvomeleze. Mwadyaidya nyama, kutengerana ku hotela nde lero mudzikanena kuti MCP ndi Chakwera ndioyipa? Ayi.

“Mupepesa bwanji mutadya kale mitanda 8, mukuona ngati mukuuza ana kapena? UTM inachokera mu DPP, munakakhala a nzeru munakakapepesa ku DPP-ko mubwelele osati kupepesa aMalawi,” watelo Kalindo.

Iye wati zamudandaulitsa kuti UTM yazindikira pano kuti zinthu sizili bwino pomwe iye m’buyomu wakhala akulangiza chipanichi kuti chichoke mu mgwirizanowu, koma wati anthu mchipanichi ankamutukwana.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.