A Namalomba akufuna umboni ngati ndani? – Suleman


Sameersuleman- Malawi24
Kwakhwithima! Ndipo mawere awirirana! Kusagwirizana kwa akuluakulu aboma kwafika mlingo wina tsopano pomwe sipikala wa nyumba yamalamulo, Sameer Suleman wabweza moto kwa a Shadric Namalomba.

“Kodi a Namalomba akufuna umboni ngati ndani? A Namalomba asanduka liti wapolisi kapena wa ACB? Awa ndi ena mwa mafunso omwe achoka kwa sipikala kupita kwa nduna yofalitsa nkhaniyi.

Chatsitsa dzaye? Masiku apitawa, a Namalomba adapereka masiku asanu ndi awiri (7) kwa a Suleman kuti abweretse umboni poyera pa nkhani yoti akuluakulu aboma ena akuchita katangale.

A Namalomba anayankhula izi potsatira zomwe a Suleman anayankhula posachedwapa pa mwambo wina wa chisilamu komwe analangiza akuluakulu aboma ena kuti asinthe kagwiridwe ntchito komaso asiye kuwabera a Malawi.

Koma pano mbuto ya kalulu yakula ndi tadzaonani: Suleman naye walavula khala lamoto. Iye wati ndizodabwitsa kuti a Namalomba anayambukira udindo wawo chonchi mpaka kufika powawerengera masiku.

Poyankhula ndi wailesi ya kanema ya Times, Suleman wati akukhulupira kuti kusadziwa malire a ntchito yawo ndikomwe kwapangitsa a Namalomba kuwafusa kuti apereke umboni pa nkhani za katangale m’boma zomwe wakhala akudzudzula.

Suleman wati ngakhale ali ndi umboni wa nkhaniyi koma sakuwona chifukwa chowapatsira a Namalomba ponena kuti nduna yofalitsa nkhaniyi si wapolisi.

“Ndine odabwa kuti Namalomba akufuna umboni ngati ndani, wasanduka liti wapolisi kapena wa ACB? Umboni ndili nawo koma atume anthu oyenera. Iwowo choyenera kuchita akuvlchidziwa,” watero Suleman.

Iwo atiso apereka umboni omwe ali nawo pokhapokha pakhale chitsimikizo kuti awugwiritsa ntchito, osati kungopereka popanda chochitika.

Suleman anapitiriza ndikudzudzula a Namalomba kamba kodumpha malire, ponena kuti pokhala mneneri wa nthambi ya boma sizikutanthauza kuti ndi mneneri wa nyumba yamalamulo yomwe ati ndi mbali inaso ya boma.

Akuluakulu a DPP awiriwa akhala akulozana dzala kwa kanthawi tsopano, kuchokera pomwe a Suleman analengeza zofuna kukhazikitsa makomiti ku nyumba yamalamulo, omwe cholinga chake chinali kufufuza katangale yemwe akuchitika m’boma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading