Wanjinga wafa pothawitsa mafuta kwa apolisi


Img 20261019 Wa0003- Malawi24

Woyendetsa njinga yamoto yemwe ananyamula zigubu zamafuta a galimoto, wafa atagwa ndikuyaka moto pomwe amathamangitsidwa ndi a polisi.

Malingana ndi yemwe tawona pa tsamba la Facebook, izi zachitika pa Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.

Mu kanemayu mukuveka mau a yemwe amajambula ndipo wafotokoza kuti wanjingayu amathawa galimoto yapolisi yomwe imamuthangitsa, koma anakagwera kutchire komwe moto unabuka.

“Pothawa a polisi, wakagwera kutchire ndipo njinga yayaka ndi munthu yemweyo wafera pomwepo,” anatero wojambulayu.

Iye wati a polisi atawona izi sanayime pamalopa angozipo ndipo pomwe anthu amafikapo moto unali utakolera kwambiri.

Izi zikudza pomwe mafuta akhala akuvuta kwambiri m’dziko, zomwe zapangitsa anthu ena kumagulitsa pa msika osavomerezeka.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading