Mneneri ankandiyamwitsa njoka — Waulura msungwana wina


Walinasechisanu- Malawi24
Pomwe mukupita kumapemphero lero, Kodi mwamva? Zaka pafupifupi khumi zapitazo, msungwana wina wotchuka ndi zisudzo pa TikTok, anagwa mchikondi ndi mneneri wa ‘mulungu’, koma mhuu! Mathero ake n’ngachabe.

Pomwe iye amanyadira kuti anali mayi pulofeti, sadadziwe kuti kukada amakhala ‘mayi chinjoka.’ Kupatula kugonana ndi munthu wa ‘mulungu’yo, mabere ake ankagwiritsidwaso ntchito zina.

Walinase Chisanu, yemwe amatchuka ndi zisudzo pa tiktok, anachimina ndipo anatsimikiza kuti sadzakhulipiraso aliyese ngakhale wopemphera pomwe mneneri wina ankamugwiritsa ntchito zakumidima.

Chisanu wawuza kanema wina kuti mu 2015 anagwa mchikondi ndi mneneri wina. Iye wati mneneriyu amati akafika m’dziko muno kuchoka ku Namibia komwe amakhala, chibwezi chawo chinkafumbira kufika mpaka amagonana.

“Utumiki wake ankachitira kwa Mwenyekondo, (Lilongwe) ndipo ankandiitana kunyumba kwake Loweruka lililonse komwe tinkagona limodzi usiku wake,” watero Chisanu.

Iye wati chomwe chinkamudabwitsa ndichoti akagona limodzi, mneneriyu ankamudzutsa 3 koloko m’bandakucha ndikumusamutsira chipinda china ponena kuti sankafuna akumpingo adziwe kuti akumagona limodzi, chonsecho panalibe waku mpingo yemwe ankapita kunyumbayi.

Chisanu wati ngakhale nkuluyu anali asanamulalikireko, koma uzimu wake unakwera kotero anafika poyamba nawo gulu la achinyamata oyimba mu utumikiwu komaso amasala kudya katatu pasabata, zomwe sizinasangalatse mneneriyu.

“Atawona uzimu wanga wakwera, anathetsa chibwezi popanda chifukwa, ndinalira mpaka ndinapita kwa mneneri wina kuti achotse satana yemwe ankasokoneza chibwezichi.”

Walinase wati anauza mneneri woyamba waku Area 18 kuti amupempherere kuchotsa chiwanda chomwe chikusokoneza ubwezi wake, koma mneneriyu anangomuyang’ana, kumudutsa osamuyankha.

Patadutsa masiku ochepa, anthu ena anatengeraso Chisale kwa mai wina wopemphera kwa Senti, yemwe anamuuza kuti mneneri uja ndiwakumidima, ndipo anamupempha kuti apeze mneneri wa mphamvu woti amuchotse mu gori lomwe analowamo.

Apa Walinase anabwereraso kwa mneneri waku Area 18 uja yemwe anamupatsa madzi, ndikumuuza kuti akasambe ndikupemphera zolimba ndipo akawona chilichonse chokhudza bwezi lake lija.

“Nditatsatira ndondomeko za mneneri uja, usiku ndinalota ndili ku utumiki wa bwezi langa lija ndipo njoka inkandiyamwa mabere, koma pambali pakeso panaliso njoka zina ziwiri. Ndinatuluka ndikulalata ndipo ndinaona mai wina ogwira ntchito komweku atatola njoka ina ndikudigendera,” watero Walinase.

Iye wati kuchoka pomwepo anasiya mpingowu, koma anayambaso kupanga chibwezi ndi m’busa wimu mpingo omwewo.

Iye wati patadutsa nthawi, anapita kwa munthu wina wopemphera yemwe anamumasulira maloto onse aja ndipo anamuuza kuti njoka ija inali bwezi lake lakalero, lomwe akuti likamagona naye limatenga m’dalitso wake, ndipo akamamusamutsa kuchipinda 3 koloko amakhala akupempherera zomwe watenga.

Munthuyu anauzaso Walinase kuti njoka ziwiri zija anali a neneri ena amu mpingowu omwe amafunaso atenge gawo lawo pogonana naye, ndipo iye wati anatsimikizadi izi poti aneneri ena a mpingowo anamufusira pomwe chibwezi chake chinali chitangotha kumene.

Ndipo za m’busa yemwe anayamba naye ubwezi atasiyana ndi mneneri uja, ati inali njoka yomwe anamuponyera ndi mai ogwira ntchito ku utumikiwu kumaloto kuja.

Walinase Chisanu wati patadutsa nthawi mneneri wakumidima uja anabwera kunyumba kwake m’maloto, ngakhale atatsitsimuka panali zizindikira zowonetsa kuti anabweradi ndipo munkubwera kwake anafofokoza mmene anayambira zakumidima ndipo analonjeza nsungwanayu K10 Miliyoni ngati angayambe nawo zakumidimazi koma Walinase anakana.

Iye anamaliza ndi chenjezo kwa aliyense kuti sikwabwino kukhulupilira aliyese, potengera kuti ngakhale atumiki amene akuchita zoopsa kwambiri.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading